bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Revelation 10
Revelation 10
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 11 →
1
Ndipo ndinaona mngelo wina wolimba alikutsika Kumwamba, wobvala mtambo; ndi utawaleza pamutu pace, ndi nkhope yace ngati dzuwa, ndi mapazi ace ngati mizati yamoto;
2
ndipo anali nako m'dzanja lace kabuku kofunyulula: ndipo anaponda nalo phazi lace lamanja panyanja,
3
ndi Iamanzerelo pamtunda, napfuula ndi mau akuru, monga ngati mkango ubangula; ndipo pamene anapfuula mabingu asanu ndi awiri analankhula mau ao.
4
Ndipo pamene adalankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndinati ndilembe; ndipo udinamva mau ocokera Kumwamba nanena, Sindikiza naco cizindikilo zimene adalankhula mabingu asanu ndi limodzi, ndipo usazilembe,
5
Ndipo mngelo amene ndinamuona alikuimirira panyanja ndi pa mtunda, anakweza dzanja lace lamanja kuloza kumwamba,
6
nalumbira kuchula iye amene ali ndi moyo ku nthawi za nthawi, amene analenga m'mwamba ndi zinthu ziri momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu ziri momwemo, ndi nyanja ndi zinthu ziri momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi:
7
komatu m'masiku a mau a mngelo wacisanu ndi ciwiri m'mene iye adzayamba kuomba, pamenepo padzatsirizika cinsinsi ca Mulungu, monga analalikira kwa akapolo ace aneneri.
8
Ndipo mau ndinawamva ocokera Kumwamba, analankhulanso nane, nanena, Muka, tenga buku lofunyululalom'dzanja la mngelo wakuimirira panyanja ndi padziko.
9
Ndipo ndinamuka kwa mngelo, ndi kunena naye, Ndipatse kabukuko. Ndipo ananena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m'mimbamwako, komatu m'kamwa mwako kadzazuna ngati uci.
10
Ndipo ndinatenga kabuku m'dzanja la mngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kanali m'kamwa mwanga kozuna ngati uci; ndipo pamene ndinakadya m'mimba mwanga mudawawa.
11
Ndipo ananena nane, Uyenera iwe kuneneranso pa anthu ndi mitundu, ndi manenedwe, ndi mafumu ambiri.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22