bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Revelation 20
Revelation 20
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 21 →
1
Ndipo ndinaona mngelo anatsika Kumwamba, nakhala naco cifungulo ca phompho, ndi unyolo waukuru m'dzanja lace.
2
Ndipo anagwira cinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nammanga iye zaka cikwi,
3
namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo cizindikilo pamwamba pace, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka cikwi; patsogolo pace ayenera kumasulidwa iye kanthawi.
4
Ndipo ndinaona mipando yacifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa ciweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi cifukwa ca umboni wa Yesu, ndi cifukwa ca mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira cirombo, kapena fano lace, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nacita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka cikwi.
5
Otsala a akufa sanakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka cikwi. Ndiko kuuka kwa akufa koyamba.
6
Wodala ndi woyera mtima ali iye amene acita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yaciwiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzacita ufumu pamodzi ndi iye zaka cikwizo.
7
Ndipo pamene zidzatha zaka cikwi, adzamasulidwa Satana m'ndende yace;
8
nadzaturuka kudzasokeretsa amitundu ali mu ngondya zinai za dziko, Gogo, ndi Magogo, kudzawasonkhanitsa acite nkhondo: ciwerengero cao ca iwo amene cikhala ngati mcenga wa kunyanja.
9
Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo: ndipo unatsika mota wakumwamba nuwanyeketsa.
10
Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya mota ndi sulfure, kumeneko kulinso ciromboco ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku ku nthawi za nthawi.
11
Ndipo ndinaona, mpando wacifumu waukuru woyera, ndi iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pace, ndipo sanapezedwamalo ao.
12
Ndipo ndinaona akufa, akuru ndi ang'ono alinkuima ku mpando wacifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina Iinatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa nchito zao.
13
Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa nchito zace,
14
Ndipo imfa ndi Hade zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yaciwiri, ndiyo nyanja yamoto.
15
Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22