bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Revelation 13
Revelation 13
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 14 →
1
Ndipo ndinaimirira pa mcenga wa nyanja. Ndipo ndinaona cirombo cirinkuturuka m'nyanja, cakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ow iwiri, ndi pa nyanga zace nduwira zacifumu khumi, ndi pamitu pace maina a mwano.
2
Ndipo cirombo ndinacionaco cinafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ace ngati mapazi a fisi, ndi pakamwa pace ngati pakamwa pa mkango; ndipo cinjoka cinampatsa iye mphamvu yace, ndi mpando wacifumu wace, ndi ulamuliro waukuru.
3
Ndipo umodzi wa mitu yace unakhala ngati unalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lace la kuimfa lidapola; ndipo dziko lonse linazizwa potsata ciromboco;
4
ndipo analambira cinjoka, cifukwa cinacipatsa ulamuliro ciromboco; ndipo analambira cirombo ndi kunena, Manana ndi cirombo ndani? Ndipo akhoza ndani kugwira nkhondo naco?
5
Ndipo anacipatsa ico m'kamwa molankhula zazikuru ndi zamwano; ndipo anacipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri.
6
Ndipo cinatsegula pakamwa pace kukanena zamwano pa Mulungu, kucitira mwano dzina lace, ndi cihema cace, ndi iwo akukhala m'Mwamba.
7
Ndipo anacipatsa ico kucita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwalaka; ndipo anacipatsa ulamuliro wa pa pfuko liri lonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.
8
Ndipo adzacilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi,
9
N gati wina ali nalo khutu, amve.
10
N gati munthu alinga kundende, kundende adzamuka munthu akapha ndi lupanga, ayenera iyekuphedwa nalo lupanga, Pano pali cipiriro ndi cikhulupiriro ca oyera mtima.
11
Ndipo ndinaona cirombo cina cirikuturuka pansi; ndipo cinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwana wa nkhosa, ndipo cinalankhula ngati cinjoka.
12
Ndipo cicita ulamuliro wonse wa cirombo coyamba pamaso pace. Ndipo cilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo cirombo coyamba, cimene bala lace la kuimfa lidapola.
13
Ndipo cicita zizindikilo zazikuru, kutinso citsitse moto ucokere m'mwamba nugwe padziko, pamaso pa anthu.
14
Ndipo cisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikilo zimene anacipatsa mphamvu yakuzicita pamaso pa cirombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fane la ciromboco, cimene cinali nalo bala la lupanga nicinakhalanso ndi moyo.
15
Ndipo anacipatsa mphamvu yakupatsa fano la cirombo mpweya, kutinso fane la cirombo Iilankhule, nilicite kuti onse osalilambira fane la cirombo aphedwe.
16
Ndipo cicita kuti onse, ang'ono ndi akuru, acuma ndi osauka, ndi mfulu ndi akapolo, alandire cilembo pa dzanja lao ndi pamphumi pao;
17
ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala naco cilembo, ndilo dzina la cirombo, kapena ciwerengero ca dzina lace.
18
Pano pali nzeru. Iye wakukhala naco cidziwitso awerenge ciwerengero ca ciromboco; pakuti ciwerengero cace ndi ca munthu; ndipo ciwerengero cace ndico mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi cimodzi.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22