bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Zechariah 2
Zechariah 2
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 3 →
1
Ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, munthu ndi cingwe coyesera m'dzanja lace.
2
Ndipo ndinati, Upita kuti? Ndipo anati kwa ine, Kukayesa Yerusalemu, kuona ngati citando cace ncotani, ndi m'litali mwace motani.
3
Ndipo taonani, mthenga wolankhula nane anaturuka, ndi mthenga wina anaturuka kukomana naye,
4
nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, M'Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, cifukwa ca kucuruka anthu ndi zoweta momwemo.
5
Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pace, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwace.
6
Haya, haya, thawani ku dziko la kumpoto, ati Yehova; pakuti ndinakubalalitsani ngati mphepo zinai za kuthambo, ati Yehova.
7
Haya Ziyoni, thawa iwe wakukhala ndi mwana wamkazi wa Babulo.
8
Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lace.
9
Pakuti, taonani, ndidzawayambasira dzanja langa, ndipo adzakhala zofunkha za iwo amene anawatumikira; ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma.
10
Yimba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndirinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova.
11
Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.
12
Ndipo Yehova adzalandira colowa cace Yuda, ngati gawo lace m'dziko lopatulikalo, nadzasankhanso Yerusalemu.
13
Khalani cete, anthu onse, pamaso pa Yehova; pakuti wagalamuka mokhalira mwace mopatulika.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14