bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Zechariah 4
Zechariah 4
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 5 →
1
Ndipo mthengayo adalankhula nane, anadzanso, nandiutsa ngati munthu woutsidwa m'tulo tace.
2
Ndipo anati kwa ine, Uona ciani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, coikapo nyali ca golidi yekha yekha, ndi mbale yace pamwamba pace, ndi nyali zace zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pace;
3
ndi mitengo iwiri yaazitona pomwepo, wina ku dzanja lamanja la mbaleyo, ndi wina ku dzanja lace lamanzere.
4
Ndipo ndinayankha ndi kunena ndi mthenga wakulankhula ndi ine, ndi kuti, Izi nziani mbuyanga?
5
Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anayankha, nati kwa ine, Sudziwa kodi kuti nziani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga.
6
Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.
7
Ndiwe yani, phiri lalikuru iwe? pamaso pa Zerubabele udzasanduka cidikha; ndipo adzaturutsa mwala wa cimbudzi, ndi kupfuula, Cisomo, cisomo nao.
8
Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti,
9
Manja a Zerubabele anaika maziko a nyumba iyi, manja ace omwe adzaitsiriza; ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makatnu anandituma kwa inu.
10
Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona cingwe colungamitsira ciriri m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse.
11
Pamenepo ndinayankha, ndinati kwa iye, Mitengo iyi iwiri ya azitona kulamanja ndi kulamanzere kwa coikapo nyali nciani?
12
Ndipo ndinayankha kaciwiri, ndinati naye, Nzotani nthambi ziwiri izi za azitona zirikutsanula zokha mafuta onga golidi mwa misiwe iwiri yagolidi?
13
Ndipo anandiyankha, nati, Sudziwa kodi kuti nziani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga.
14
Pamenepo anati, Awa ndi ana amuna awiri a mafuta oimirira pamaso pa Mbuye wa dziko lonse lapansi.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14