bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Zechariah 9
Zechariah 9
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 10 →
1
Katundu wa mau a Yehova pa dziko la Hadraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pace; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israyeli;
2
ndi Hamati yemwe wogundana naye malire; Turo ndi Zidoni, angakhale ali ndi nzeru zambiri.
3
Ndipo Turo adzadzimangira polimbikirapo, nadzakundika siliva ngati pfumbi, ndi golidi woyenga ngati thope la kubwalo.
4
Taonani, Yehova adzamlanda zace, nadzakantha mphamvu yace igwe m'manja; ndipo adzatha ndi moto.
5
Asikeloni adzaciona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekroni, pakuti ciyembekezo cace cacitidwa manyazi; ndipo mfumu idzatayika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo.
6
Ndi mtundu wa anthu osokonezeka udzakhala m'Asidodi, ndipo ndidzaononga kudzikuza kwa Afilisti.
7
Ndipo ndidzacotsa mwazi wace m'kamwa mwace, ndi zonyansa zace pakati pa mano ace; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkuru wa pfuko m'Yuda, ndi Ekroni ngati Myebusi.
8
Ndipo ndidzamangira nyumba yanga misasa, kuiletsera nkhondo, asapitepo munthu kapena kubweranso; ndipo wakuwasautsa sadzapitanso pakati pao; pakuti tsopano ndapenya ndi maso anga.
9
Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; pfuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini cipulumutso; wofatsa ndi wokwera pa buru, ndi mwana wamphongo wa buru.
10
Ndipo ndidzaononga magareta kuwacotsa m'Efraimu, ndi akavalo kuwacotsa m'Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wace udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.
11
Iwenso, cifukwa ca mwazi wa pangano lako ndinaturutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi.
12
Bwererani kudza kulinga, andende a ciyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera cowirikiza.
13
Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efraimu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi.
14
Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi mubvi wace udzaturuka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akabvumvulu a kumwela.
15
Yehova wa makamu adzawacinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzacita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngondya za guwa la nsembe.
16
Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ace; pakuti adzakhala ngati miyala ya m'korona yakunyezimira pa dziko lace.
17
Pakuti ukoma wace ndi waukuru ndithu, ndi kukongola kwace nkwa kukuru ndithu! tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14