bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Amos 3
Amos 3
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 4 →
1
Tamverani mau awa akunenerani Yehova motsutsa, inu ana a Israele, kulinenera banja lonse ndinalikweza kulitulutsa m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
2
Inu nokha ndinakudziwani mwa mabanja onse a pa dziko lapansi, m'mwemo ndidzakulangani chifukwa cha mphulupulu zanu zonse.
3
Kodi awiri adzayenda pamodzi asanapanganiranetu?
4
Kodi mkango udzabangula m'nkhalango wosakhala nayo nyama? Kodi msona wa mkango udzalira m'ngaka mwake usanagwire kanthu?
5
Kodi mbalame idzakodwa mumsampha pansi popanda msampha woitchera? Kodi msampha ufwamphuka pansi wosakola kanthu?
6
Kodi adzaomba lipenga m'mudzi osanjenjemera anthu? Kodi choipa chidzagwera mudzi osachichita Yehova?
7
Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.
8
Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?
9
Bukitsani kunyumba zachifumu za Asidodi, ndi kunyumba zachifumu za m'dziko la Ejipito, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero akulu m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwake.
10
Pakuti sadziwa kuchita zolungama, amene akundika zachiwawa ndi umbala m'nyumba zao zachifumu, ati Yehova.
11
Chifukwa chake, atero Ambuye Yehova, Padzakhala mdani pozungulira pake pa dziko, nadzatsitsa kukuchotsera mphamvu yako; ndi za m'nyumba zako zachifumu adzazifunkha.
12
Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israele okhala pansi m'Samariya, m'ngodya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama.
13
Tamverani inu, muchitire umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo, ati Ambuye Yehova Mulungu wa makamu.
14
Pakuti tsiku lakumlanga Israele chifukwa cha zolakwa zake, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Betele; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, nizidzagwa pansi.
15
Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuluzo zidzatha, ati Yehova.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9