bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Amos 4
Amos 4
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 5 →
1
Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe.
2
Ambuye Yehova walumbira pali chiyero chake, kuti taonani, adzakugwerani masiku akuti adzakuchotsani ndi zokowera, ndi otsala anu ndi mbedza.
3
Ndipo mudzatulukira popasuka linga, yense m'tsogolo mwake, ndi kutayika ku Harimoni, ati Yehova.
4
Idzani ku Betele, mudzalakwe ku Giligala, nimuchulukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m'mawa ndi m'mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatuatatu;
5
nimutenthe nsembe zolemekeza zachotupitsa, nimulalikire nsembe zaufulu, ndi kuzimveketsa; pakuti ichi muchikonda, inu ana a Israele, ati Ambuye Yehova.
6
Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'midzi yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.
7
Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mudzi umodzi mvula, osavumbitsira mudzi wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota.
8
M'mwemo midzi iwiri kapena itatu inayenda peyupeyu kumudzi umodzi kukamwa madzi, koma sanakhute; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.
9
Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni; minda yanu yochuluka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi ya azitona, yaonongeka ndi dzombe; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.
10
Ndinatumiza mliri pakati panu monga m'Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.
11
Ndinagubuduza ena mwa inu, monga umo Mulungu anagubuduzira Sodomu ndi Gomora; ndipo inu munali ngati muuni wofumulidwa kumoto; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.
12
Chifukwa chake ndidzatero nawe, Israele; popeza ndidzakuchitira ichi, dzikonzeretu kukomana ndi Mulungu wako, Israele.
13
Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9