bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Amos 5
Amos 5
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 6 →
1
Tamverani mau awa ndinenawa, akhalire inu nyimbo ya maliro, nyumba ya Israele inu.
2
Namwali wa Israele wagwa, sadzaukanso; wagwetsedwa pa nthaka yake, palibe womuutsa.
3
Pakuti atero Ambuye Yehova, M'nyumba ya Israele, mudzi wotulukamo chikwi chimodzi adzautsalira zana limodzi, ndi uwu wotulukamo zana limodzi adzautsalira khumi.
4
Pakuti atero Yehova kwa nyumba ya Israele, Mundifunefune Ine, ndipo mudzakhala ndi moyo;
5
koma musamafuna Betele, kapena kumalowa m'Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.
6
Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi moyo; angabuke ngati moto m'nyumba ya Yosefe, ndipo unganyeke wopanda wakuzima m'Betele;
7
inu osintha chiweruzo chikhale chivumulo, nimugwetsa pansi chilungamo.
8
Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira pa dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova;
9
wakufikitsa chionongeko pa wamphamvu modzidzimuka, chionongeko nichigwera linga.
10
Iwo adana naye wodzudzula kuchipata, nanyansidwa naye wolunjikitsa mau.
11
Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsokhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wake.
12
Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzochuluka, ndi machimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira chokometsera mlandu, akukankha osowa kuchipata.
13
Chifukwa chake wochenjerayo akhala chete nthawi yomweyo; pakuti ndiyo nthawi yoipa.
14
Funani chokoma, si choipa ai; kuti mukhale ndi moyo; motero Yehova Mulungu wa makamu adzakhala ndi inu, monga munena.
15
Danani nacho choipa, nimukonde chokoma; nimukhazikitse chiweruzo kuchipata; kapena Yehova Mulungu wa makamu adzachitira chifundo otsala a Yosefe.
16
Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! Kalanga ine! Nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire.
17
Ndi m'minda yonse yamipesa mudzakhala kulira, pakuti ndipita pakati pako, ati Yehova.
18
Tsoka inu akufuna tsiku la Yehova? Mudzapindulanji nalo tsiku la Yehova? Ndilo mdima, si kuunika ai.
19
Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi chimbalangondo chikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lake, nimluma njoka.
20
Kodi tsiku la Yehova silidzakhala la mdima, si la kuunika ai? Lakuda bii, lopanda kuwala m'menemo?
21
Ndidana nao, ndinyoza zikondwerero zanu, sindidzakondwera nao masonkhano anu oletsa.
22
Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine.
23
Mundichotsere phokoso la nyimbo zanu; sindifuna kumva mayimbidwe a zisakasa zanu.
24
Koma chiweruzo chiyende ngati madzi, ndi chilungamo ngati mtsinje wosefuka.
25
Ngati munabwera nazo kwa Ine nsembe zophera ndi zaufa zaka makumi anai m'chipululu, inu nyumba ya Israele?
26
Inde mwasenza hema wa mfumu yanu, ndi tsinde la mafano anu, nyenyezi ya mulungu wanu, amene mudadzipangira.
27
M'mwemo ndidzakutengani kunka nanu kundende kutsogolo kwa Damasiko, ati Yehova, amene dzina lake ndiye Mulungu wa makamu.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9