bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Isaiah 22
Isaiah 22
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 23 →
1
Katundu wa chigwa cha masomphenya. Mwatani kuti mwakwera nonsenu pamachindwi?
2
Iwe amene wadzala ndi zimfuu, mudzi waphokoso, mudzi wokondwa; ophedwa ako sanaphedwe ndi lupanga, sanafe m'nkhondo.
3
Olamulira ako onse athawa pamodzi, anamangidwa ndi amauta; opezedwa ako onse anamangidwa pamodzi, nathawira patali.
4
Chomwecho ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, chifukwa cha kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.
5
Pakuti nditsiku laphokoso, ndi lopondereza pansi, ndi lothetsa nzeru, lochokera kwa Ambuye Yehova wa makamu, m'chigwa cha masomphenya, kugumuka kwa malinga, ndi kufuulira kumapiri.
6
Ndipo Elamu anatenga phodo, ndi magaleta a anthu ndi apakavalo; ndipo Kiri anaonetsa zikopa.
7
Ndipo panali kuti zigwa zako zosankhika zinadzala magaleta, ndi apakavalo anadzinika okha pachipata.
8
Ndipo Iye anachotsa chophimba cha Yuda; ndipo iwe unayang'ana tsiku limenelo pa zida za m'nyumba ya nkhalango.
9
Ndipo inu munaona kuti pa mudzi wa Davide panagumuka mipata yambiri; ndipo munasonkhanitsa pamodzi madzi a m'thamanda lakunsi.
10
Ndipo inu munawerenga nyumba za Yerusalemu, ndipo munagwetsa nyumba, kuti mumangire linga.
11
Inu munapanganso chosungamo madzi a thamanda lakale, pakati pa malinga awiri; koma inu simunamuyang'ane iye amene anachichita icho, ngakhale kusamalira iye amene analipanga kale.
12
Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kuvala chiguduli m'chuuno;
13
koma taonani, kukondwa, ndi kusekerera, ndi kupha ng'ombe, ndi kupha nkhosa, ndi kudya nyama, ndi kumwa vinyo; tiyeni tidye ndi kumwa, chifukwa mawa tidzafa.
14
Ndipo Yehova wa makamu wadzivumbulutsa yekha m'makutu mwanga, Ndithu choipa chimenechi sichidzachotsedwa pa inu kufikira inu mudzafa, ati Ambuye, Yehova wa makamu.
15
Atero Ambuye Yehova wa makamu, Muka, pita iwe kwa kapitao uyu, kwa Sebina woyang'anira nyumba, ndi kuti,
16
Uchitanji iwe kuno, ndimo ndani ali nawe kuno, kuti iwe wagoba manda kuno, ndi kudzigobera manda pamwamba, ndi kudzisemera mogonamo m'thanthwe.
17
Taona Yehova adzakuponya iwe zolimba, monga mwamuna wamphamvu, inde adzakufumbata zolimba.
18
Iye ndithu adzakuzunguza, ndi kukuponyaponya ngati mpira m'dziko lalikulu; kumeneko iwe udzafa, ndipo kumeneko kudzakhala magaleta a ulemerero wako, iwe wochititsa manyazi banja la mbuye wako.
19
Ndipo Ine ndidzakutulutsa iwe mu ntchito yako, ndi kukutsitsa iwe pokhala pako.
20
Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Ine ndidzaitana mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya:
21
ndipo ndidzamveka iye chovala chako, ndi kumlimbikitsa ndi lamba lako, ndipo ndidzapereka ulamuliro wako m'dzanja lake; ndipo iye adzakhala atate wa okhala m'Yerusalemu ndi a nyumba ya Yuda.
22
Ndipo ndidzaika mfungulo wa nyumba ya Davide paphewa pake, ndipo iye adzatsegula, ndipo palibe wina adzatseka, iye adzatseka ndipo palibe wina adzatsegula.
23
Ndipo ndidzamkhomera iye ngati chikhomo cholimba; ndipo iye adzakhala mpando wa ulemerero wa banja la atate wake.
24
Ndipo iwo adzapachika pa iye ulemerero wonse wa banja la atate wake, obadwa ndi ana, mbiya zonse zazing'ono, ngakhale zikho ndi aguda omwe.
25
Tsiku limenelo, ati Yehova wa makamu, chikhomo chokhomeredwa polimba udzasukusika; nudzaguluka, ndi kugwa, ndi katundu wopachikidwapo adzadulidwa; pakuti Yehova wanena.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66