bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Isaiah 32
Isaiah 32
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 33 →
1
Taonani mfumu idzalamulira m'chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m'chiweruzo.
2
Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.
3
Ndipo maso a iwo amene aona sadzatsinzina, ndi makutu a iwo amene amva adzamvera.
4
Mtimanso wansontho udzadziwa nzeru, ndi lilime la achibwibwi lidzalankhula zomveka msanga.
5
Wopusa sadzayesedwanso woolowa manja, ngakhale wouma manja sadzayesedwa mfulu.
6
Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.
7
Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.
8
Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe.
9
Ukani, akazi inu, amene mulinkukhala phee, mumve mau anga; inu ana akazi osasamalira, tcherani makutu pa kulankhula kwanga.
10
Pakutha chaka, kudza masiku ena inu mudzavutidwa, inu akazi osasamalira; pakuti masika a mphesa adzasoweka, sadzatuta konse.
11
Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhalaphe; vutidwani, inu osasamalira, vulani mukhale maliseche, nimumange chiguduli m'chuuno mwanu.
12
Iwo adzadzimenya pazifuwa chifukwa cha minda yabwino, chifukwa cha mpesa wobalitsa.
13
Pa dziko la anthu anga padzafika minga ndi lunguzi; inde pa nyumba zonse zokondwa, m'mudzi wokondwerera;
14
pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mudzi wa anthu ambiri udzakhala bwinja; chitunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba kunthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta;
15
kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kuchokera kumwamba, ndi chipululu chidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.
16
Pamenepo chiweruzo chidzakhala m'chipululu, ndi chilungamo chidzakhala m'munda wobalitsa.
17
Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.
18
Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.
19
Koma kudzagwa matalala m'kugwa kwake kwa nkhalango; ndipo mudzi udzagwetsedwa ndithu.
20
Odala muli inu, amene mubzala m'mbali mwa madzi monse, amene muyendetsa mapazi a ng'ombe ndi bulu.
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 33 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66