bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Isaiah 48
Isaiah 48
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 49 →
1
Imvani inu ichi, banja la Yakobo, amene mutchedwa ndi dzina la Israele, amene munatuluka m'madzi a Yuda amene mulumbira dzina la Yehova ndi kutchula dzina la Mulungu wa Israele, koma si m'zoona, pena m'chilungamo.
2
Pakuti adziyesa okha a mudzi wopatulika, ndi kudzikhazikitsa iwo okha pa Mulungu wa Israele; dzina lake ndi Yehova wa makamu.
3
Ndanena zinthu zoyamba kuyambira kale; inde, izo zinatuluka m'kamwa mwanga, ndipo ndinazisonyeza; mwadzidzidzi ndinazichita izo, ndipo zinaoneka.
4
Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako lili mtsempha wachitsulo, ndi mphumi yako mkuwa;
5
chifukwa chake ndinakudziwitsa ichi kuyambira kale; chisanaoneke ndinakusonyeza icho, kuti iwe unganene, Fano langa lachita izo, ndi chifaniziro changa chosema, ndi chifaniziro changa choyenga zinazilamulira.
6
Iwe wachimva; taona zonsezi; ndipo inu kodi inu simudzachinena? Ndakusonyeza iwe zinthu zatsopano kuchokera nthawi yino, ngakhale zinthu zobisika, zimene iwe sunazidziwe.
7
Zalengedwa tsopano, zosati kuyambira kale; ndipo lisanafike tsiku laleroli iwe sunazimve; unganene, Taonani, ndinazidziwa.
8
Inde, iwe sunamva; inde, sunadziwe; inde kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wachita mwachiwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa chibadwire.
9
Chifukwa cha dzina langa ndidzachedwetsa mkwiyo wanga, ndi chifukwa cha kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakuchotse.
10
Taona ndakuyenga, koma si monga siliva, ndakuyesa iwe m'ng'anjo ya masautso.
11
Chifukwa cha Ine ndekha, chifukwa cha Ine ndekha ndidzachita ichi, pakuti dzina langa lidetsedwerenji? Ndi ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina.
12
Mverani Ine, Yakobo ndi Israele, oitanidwa anga, Ine ndine; ndine woyamba, Inenso ndine womaliza.
13
Inde dzanja langa linakhazika maziko a dziko lapansi, ndi dzanja langa lamanja linafunyulula m'mwamba; pakuziitana Ine ziimirira pamodzi.
14
Sonkhanani inu nonse ndi kumva, ndani mwa iwo aonetsa zinthu izi? Iye amene Yehova anamkonda, iye adzachita kufuna kwake pa Babiloni, ndi mkono wake udzakhala pa Ababiloni.
15
Ine, ngakhale Ine ndanena; inde ndamwitana iye, ndamfikitsa, ndipo adzapindula nayo njira yake.
16
Idzani inu chifupi ndi Ine, imvani ichi; kuyambira pa chiyambi sindinanene m'tseri; chiyambire zimenezi, Ine ndilipo; ndipo tsopano Ambuye Mulungu wanditumiza Ine ndi mzimu wake.
17
Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.
18
Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja;
19
mbeu yakonso ikadakhala monga mchenga, ndi obadwa a m'chuuno mwako momwemo; dzina lake silikadachotsedwa, pena kuonongeka pamaso panga.
20
Tulukani inu m'Babiloni, athaweni Ababiloni; ndi mau akuimba nenani inu, bukitsani ichi, lalikirani ichi, ngakhale ku malekezero a dziko; nenani, Yehova waombola mtumiki wake Yakobo.
21
Ndipo iwo sanamve ludzu, pamene Iye anawatsogolera m'mapululu; anawatulutsira madzi kutuluka m'matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika.
22
Kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa.
← Chapter 47
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 49 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66