bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Judges 10
Judges 10
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 11 →
1
Atafa Abimeleki, anauka kupulumutsa Israele Tola mwana wa Puwa, mwana wa Dodo munthu wa Isakara; nakhala iye m'Samiri ku mapiri a Efuremu.
2
Ndipo anaweruza Israele zaka makumi awiri ndi zitatu, nafa, naikidwa m'Samiri.
3
Atafa iye, anauka Yairi Mgiliyadi, naweruza Israele zaka makumi awiri mphambu ziwiri.
4
Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu okwera pa ana a abulu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo midzi makumi atatu, otchedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Giliyadi.
5
Nafa Yairi, naikidwa m'Kamoni.
6
Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala, ndi Aasitaroti, ndi milungu ya Aramu, ndi milungu ya Sidoni, ndi milungu ya Mowabu, ndi milungu ya ana a Amoni, ndi milungu ya Afilisti; ndipo anamleka Yehova osamtumikira.
7
Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, nawagulitsa m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la ana a Amoni.
8
Ndipo anaphwanya napsinja ana a Israele chaka chija, natero ndi ana onse a Israele okhala tsidya lija la Yordani m'dziko la Aamori, ndilo Giliyadi, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu.
9
Ndipo ana a Amoni anaoloka Yordani kuthiranso nkhondo Yuda ndi Benjamini, ndi nyumba ya Efuremu; napsinjika kwambiri Israele.
10
Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova ndi kuti, Takuchimwirani, popeza tasiya Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.
11
Ndipo Yehova anati kwa ana a Israele, Kodi sindinakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa Aamori, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti?
12
Asidoni omwe, ndi Aamaleke, ndi Amaoni anakupsinjani. Pamenepo munafuula kwa Ine, ndipo ndinakupulumutsani m'dzanja lao.
13
Koma mwandisiya Ine ndi kutumikira milungu ina, chifukwa chake sindikupulumutsaninso.
14
Mukani ndi kufuulira kwa milungu munaisankha, ikupulumutseni nyengo ya kusauka kwanu.
15
Koma ana a Israele anati kwa Yehova, Tachimwa, mutichitire monga mwa zonse zikomera pamaso panu; komatu mutipulumutse lero lino, tikupemphani.
16
Pamenepo anachotsa milungu yachilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wake unagwidwa chisoni chifukwa cha mavuto a Israele.
17
Ndipo ana a Amoni analalikiridwa, namanga misasa m'Giliyadi. Ndi ana a Israele anasonkhana namanga misasa ku Mizipa.
18
Ndipo anthu, akalonga a Giliyadi, ananenana wina ndi mnzake, Ndaniyo adzayamba kulimbana ndi ana a Amoni? Iye adzakhala mkulu wa onse okhala m'Giliyadi.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21