bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Judges 17
Judges 17
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 18 →
1
Ndipo ku mapiri a Efuremu kunali munthu dzina lake ndiye Mika.
2
Ndipo iye anati kwa amai wake, Ndalama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m'makutu mwanga, taonani ndalamazo ndili nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wake anati, Yehova adalitse mwana wanga.
3
Nabwezera amake ndalama zija mazana khumi ndi limodzi; nati amai wake, Kupatula ndapatulira Yehova ndalamazo zichoke ku dzanja langa, zimuke kwa mwana wanga, kupanga nazo fano losema ndi fano loyenga; m'mwemo ndikubwezera izi.
4
Ndipo pamene anambwezera mai wake ndalamazo, mai wake anatapako ndalama mazana awiri, nazipereka kwa woyenga, ndiye anazipanga fano losema ndi fano loyenga; ndipo linakhala m'nyumba ya Mika.
5
Koma munthuyu Mika anali nayo nyumba ya milungu, napanga chovala cha wansembe, ndi timafano, namninkha zansembe mwana wake wina wamwamuna, amene anakhala wansembe wake.
6
Masikuwa panalibe mfumu m'Israele, yense anachita chomuyenera m'maso mwake.
7
Ndipo panali mnyamata wa ku Betelehemu-Yuda wa banja la Yuda, ndiye Mlevi, nagonera iye komweko.
8
Adachokera munthuyo m'mudzi m'Betelehemu-Yuda, kugonera paliponse akapeza pokhala; ndi pa ulendo wake anafika ku mapiri a Efuremu, kunyumba ya Mika.
9
Ndipo Mika ananena naye, Ufumira kuti? Nati kwa iye, Ndine Mlevi wa ku Betelehemu-Yuda, ndilikumuka kugonera kumene ndikapeza pokhala.
10
Nanena naye Mika, Khalitsa nane, nukhale atate wanga, ndi wansembe wanga, ndipo ndidzakupatsa ndalama khumi pachaka, ndi chovala chofikira, ndi zakudya zako. Nalowa Mleviyo.
11
Ndi Mleviyo anavomera kukhalitsa ndi munthuyo; ndi mnyamatayo anamkhalira ngati mmodzi wa ana ake.
12
Ndipo Mika anamninkha zansembe Mleviyo, ndi mnyamatayo anakhala wansembe wake, nakhala m'nyumba ya Mika.
13
Nati Mika, Tsopano ndidziwa kuti Yehova adzandichitira chokoma, popeza ndili naye Mlevi akhale wansembe wanga.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21