bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Judges 12
Judges 12
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 13 →
1
Pamenepo amuna a Efuremu analalikidwa, napita kumpoto; nati kwa Yefita, Wapitiriranji kuthira nkhondo ana a Amoni, osatiitana ife timuke nawe? Tidzakutenthera nyumba yako ndi moto pamtu pako.
2
Ndipo Yefita anati kwa iwo, Ine ndi anthu anga tinatsutsana kwakukulu ndi ana a Amoni, koma pamene ndinakuitanani inu simunandipulumutsa m'dzanja lao.
3
Ndipo pakuona ine kuti simundipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundichitira nkhondo?
4
Pamenepo Yefita anamemeza amuna onse a m'Giliyadi nalimbana naye Efuremu; ndipo amuna a Giliyadi anakantha Efuremu, chifukwa adati, Inu Agiliyadi ndinu akuthawa Efuremu, pakati pa Efuremu ndi pakati pa Manase.
5
Ndipo Agiliyadi anatsekereza madooko a Yordani a Efuremu; ndipo kunatero kuti, akati othawa a Efuremu, Ndioloke, amuna a Giliyadi anati kwa Iye, Ndiwe Mwefuremu kodi? Akati, Iai;
6
pamenepo anati kwa iye, Unene tsono Shiboleti; ndipo akati, Siboleti, osakhoza kutchula bwino, amgwira namupha padooko pomwe pa Yordani; ndipo anagwa a Efuremu nthawi ija, zikwi makumi anai mphambu ziwiri.
7
Ndipo Yefita anaweruza Israele zaka zisanu ndi chimodzi; nafa Yefita Mgiliyadi, naikidwa m'mudzi wina wa Giliyadi.
8
Ndi pambuyo pake Ibizani wa ku Betelehemu anaweruza Israele.
9
Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu; ndi ana akazi makumi atatu anawakwatitsa kwina, natengera ana ake amuna ana akazi makumi atatu ochokera kwina. Ndipo anaweruza Israele zaka zisanu ndi ziwiri.
10
Nafa Ibizani naikidwa ku Betelehemu.
11
Ndi pambuyo pake Eloni Mzebuloni anaweruza Israele; naweruza Israele zaka khumi.
12
Nafa Eloni Mzebuloni naikidwa m'Ayaloni m'dziko la Zebuloni.
13
Ndi pambuyo pake Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni anaweruza Israele.
14
Ndipo anali nao ana amuna makumi anai ndi zidzukulu zazimuna makumi atatu, akuyenda okwera pa ana a abulu makumi asanu ndi awiri; naweruza Israele zaka zisanu ndi zitatu.
15
Nafa Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni, naikidwa m'Piratoni m'dziko la Efuremu ku mapiri a Amaleke.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21