bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Mark 1
Mark 1
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 2 →
1
Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu.
2
Monga mwalembedwa m'Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu.
3
Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.
4
Yohane anadza nabatiza m'chipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku chikhululukiro cha machimo.
5
Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao.
6
Ndipo Yohane anavala ubweya wa ngamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake, nadya dzombe ndi uchi wa kuthengo.
7
Ndipo analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula lamba la nsapato zake ine.
8
Ndakubatizani inu ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.
9
Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane m'Yordani.
10
Ndipo pomwepo, alimkukwera potuluka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda:
11
ndipo mau anatuluka m'thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.
12
Ndipo pomwepo Mzimu anamkakamiza kunka kuchipululu.
13
Ndipo anakhala m'chipululu masiku makumi anai woyesedwa ndi Satana; nakhala ndi zilombo, ndipo angelo anamtumikira.
14
Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu,
15
nanena, Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani Uthenga Wabwino.
16
Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andrea, mbale wake wa Simoni, alinkuponya khoka m'nyanja; pakuti anali asodzi.
17
Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.
18
Ndipo pomwepo anasiya makoka ao, namtsata Iye.
19
Ndipo atapita patsogolo pang'ono, anaona Yakobo, mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, iwonso anali m'chombo nakonza makoka ao.
20
Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedeo m'chombomo pamodzi ndi antchito olembedwa, namtsata.
21
Ndipo iwo analowa m'Kapernao; ndipo pomwepo pa tsiku la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa.
22
Ndipo anazizwa ndi chiphunzitso chake; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi.
23
Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anafuula iye.
24
Kuti, Tili ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife: Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.
25
Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli chete, nutuluke mwa iye.
26
Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kufuula ndi mau akulu, unatuluka mwa iye.
27
Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ichi nchiyani? Chiphunzitso chatsopano! Ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye.
28
Ndipo mbiri yake inabuka pompaja kudziko lonse la Galileya lozungulirapo.
29
Ndipo pomwepo, potuluka m'sunagoge, iwo analowa m'nyumba ya Simoni ndi Andrea pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane.
30
Ndipo mpongozi wake wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za iye:
31
ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.
32
Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda.
33
Ndipo mudzi wonse unasonkhana pakhomo.
34
Ndipo anachiritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundumitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalole ziwandazo zilankhule, chifukwa zinamdziwa Iye.
35
Ndipo m'mawa mwake anauka usikusiku, natuluka namuka kuchipululu, napemphera kumeneko.
36
Ndipo Simoni ndi anzake anali naye anamtsata,
37
nampeza, nanena naye, Akufunani Inu anthu onse.
38
Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, kumidzi ili pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera ntchito imene.
39
Ndipo analowa m'masunagoge mwao m'Galileya monse, nalalikira, natulutsa ziwanda.
40
Ndipo anadza kwa Iye wodwala khate, nampempha Iye, namgwadira, ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza.
41
Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.
42
Ndipo pomwepo khate linamchoka, ndipo anakonzedwa.
43
Ndipo anamuuzitsa, namtulutsa pomwepo,
44
nanena naye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu aliyense: koma muka, ukadzionetse kwa wansembe, nupereke pa makonzedwe ako zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo.
45
Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanadziwa kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16