bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Mark 7
Mark 7
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 8 →
1
Ndipo anasonkhana kwa Iye Afarisi, ndi alembi ena, akuchokera ku Yerusalemu,
2
ndipo anaona kuti ophunzira ake ena anadya mkate ndi m'manja mwakuda, ndiwo osasamba.
3
Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu;
4
ndipo pakuchoka kumsika, sakudya osasamba m'thupi; ndipo zilipo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa.
5
Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda?
6
Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao, koma mtima wao ukhala kutali ndi Ine.
7
Koma andilambira Iye kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.
8
Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu.
9
Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu.
10
Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo iye wakunenera zoipa atate wake kapena amai wake, afe ndithu;
11
koma inu munena, Munthu akati kwa atate wake, kapena amai wake, Korban, ndiko kuti Mtulo, chimene ukadathandizidwa nacho ndi ine,
12
simulolanso kumchitira kanthu atate wake kapena amai wake;
13
muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita.
14
Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani:
15
kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.
17
Ndipo m'mene Iye adalowa m'nyumba kusiyana ndi khamulo, ophunzira ake anamfunsa Iye fanizolo.
18
Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;
19
chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma m'mimba mwake, ndipo katulukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse.
20
Ndipo anati, Chotuluka mwa munthu ndicho chidetsa munthu.
21
Pakuti m'kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere,
22
zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:
23
zoipa izi zonse zituluka m'kati, nizidetsa munthu.
24
Ndipo Iye anauka nachoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Tiro ndi Sidoni. Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoze kubisika.
25
Koma pomwepo mkazi, kabuthu kake kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake.
26
Koma mkaziyo anali Mgriki, mtundu wake Msiro-Fenisiya. Ndipo anampempha Iye kuti atulutse chiwanda m'mwana wake.
27
Ndipo ananena naye, Baleka, athange akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana, ndi kuutayira tiagalu.
28
Koma iye anavomera nanena ndi Iye, Ine Ambuye; tingakhale tiagalu ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana.
29
Ndipo anati kwa iye, Chifukwa cha mau amene, muka; chiwanda chatuluka m'mwana wako wamkazi.
30
Ndipo anachoka kunka kunyumba kwake, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi chiwanda chitatuluka.
31
Ndipo anatulukanso m'maiko a ku Tiro, nadzera pakati pa Sidoni, kufikira ku nyanja ya Galileya, ndi kupyola pakati pa maiko a ku Dekapoli.
32
Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wachibwibwi; ndipo anampempha Iye kuti aike dzanja pa iye.
33
Ndipo anampatula pa khamu la anthu pa yekha, nalonga zala zake m'makutu mwake, nalavula malovu, nakhudza lilime lake:
34
nagadamira kumwamba, nausa moyo, nanena naye, Efata, ndiko, Tatseguka.
35
Ndipo makutu ake anatsegula, ndi chomangira lilime lake chinamasulidwa, ndipo analankhula chilunjikire.
36
Ndipo anawalamulira kuti asauze munthu aliyense; koma monga momwe Iye anawalamulitsa momwenso makamaka analalikira kopambana.
37
Ndipo anadabwa kwakukulukulu, nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16