bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Mark 3
Mark 3
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 4 →
1
Ndipo analowanso m'sunagoge; ndipo munali munthu m'menemo ali ndi dzanja lake lopuwala.
2
Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamchiritsa tsiku la Sabata; kuti ammange mlandu.
3
Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati.
4
Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchita zabwino, kapena zoipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala chete.
5
Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.
6
Ndipo Afarisi anatuluka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye.
7
Ndipo Yesu anachokako pamodzi ndi ophunzira ake nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi a ku Yudeya,
8
ndi a ku Yerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Yordani, ndi a kufupi ku Tiro ndi Sidoni, khamu lalikulu, pakumva zazikuluzo anazichita, linadza kwa Iye.
9
Ndipo anati kwa ophunzira ake, kuti kangalawa kamlinde Iye, chifukwa cha khamulo, kuti angamkanikize Iye,
10
pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze.
11
Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.
12
Ndipo anailimbitsira mau kuti isamuulule Iye.
13
Ndipo anakwera m'phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye.
14
Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira,
15
ndi kuti akhale nao ulamuliro wakutulutsa ziwanda.
16
Ndipo Simoni anamutcha Petro;
17
ndi Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo, iwo anawatcha Boaneje, ndiko kuti, Ana a bingu;
18
ndi Andrea, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani,
19
ndi Yudasi Iskariote, ndiye amene anampereka Iye.
20
Ndipo anthu ambiri anasonkhananso, kotero kuti sanathe iwo konse kudya.
21
Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka.
22
Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda.
23
Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kutulutsa Satana?
24
Ndipo ufumu ukagawanika pa uwu wokha, sukhoza kukhazikika.
25
Ndipo nyumba ikagawanika pa iyo yokha, sikhoza kukhazikika nyumbayo,
26
Ndipo Satana akadziukira mwini yekha, nagawanika, sakhoza kukhazikika, koma atsirizika.
27
Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nyumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ake, koma athange wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwake.
28
Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa machimo onse a ana a anthu, ndi zamwano zilizonse adzachita mwano nazo;
29
koma aliyense adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anapalamuladi tchimo losatha;
30
pakuti adanena, Ali ndi mzimu wonyansa.
31
Ndipo anadza amake ndi abale ake; naima kunja, namtumira uthenga kumuitana.
32
Ndipo anthu ambiri anakhala pansi pomzinga; nanena kwa Iye, Onani, amanu ndi abale anu ali kunja akufunani Inu.
33
Ndipo anawayankha nanena, Amai wanga ndi abale anga ndani?
34
Ndipo anawaunguzaunguza iwo akumzingawo, nanena, Taonani, amai wanga ndi abale anga.
35
Pakuti aliyense achita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16