bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Matthew 20
Matthew 20
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 21 →
1
Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m'munda wake wampesa.
2
Ndipo pamene adapangana ndi antchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza kumunda wake.
3
Ndipo anatuluka dzuwa litakwera, naona ena ataima chabe pabwalo;
4
ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani chimene chili choyenera. Ndipo iwo anapita.
5
Ndiponso anatuluka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nachita chimodzimodzi.
6
Ndipo poyandikira madzulo anatuluka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse chabe?
7
Iwo ananena kwa iye, Chifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa.
8
Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wake, Kaitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omalizira kufikira kwa oyamba.
9
Ndipo pamene iwo olembedwa poyandikira madzulo anadza, analandira munthu aliyense rupiya latheka limodzi.
10
Ndipo m'mene oyamba anadza, analingalira kuti adzalandira kopambana, ndipo iwonso analandira onse rupiya latheka.
11
Koma m'mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja,
12
nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake.
13
Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangana ndi ine pa rupiya latheka limodzi?
14
Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe.
15
Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?
16
Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.
17
Ndipo pamene Yesu analikukwera ku Yerusalemu, anatenga ophunzira khumi ndi awiri napita nao pa okha, ndipo panjira anati kwa iwo,
18
Onani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa,
19
nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.
20
Pomwepo anadza kwa Iye amake a ana a Zebedeo ndi ana ake omwe, namgwadira, ndi kumpempha kanthu.
21
Ndipo Iye anati kwa iye, Ufuna chiyani? Iye ananena, Lamulirani kuti ana anga awiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, mu ufumu wanu.
22
Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza.
23
Iye ananena kwa iwo, Chikho changa mudzamweradi; koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.
24
Ndipo m'mene khumiwo anamva, anapsa mtima ndi abale awiriwo.
25
Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akulu ao amachita ufumu pa iwo.
26
Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;
27
ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu:
28
monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.
29
Ndipo pamene iwo analikutuluka m'Yeriko, khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye.
30
Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m'mphepete mwa njira; m'mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anafuula nati, Mutichitire ife chifundo, Inu Mwana wa Davide.
31
Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, mutichitire chifundo, Inu Mwana wa Davide.
32
Ndipo Yesu anaima, nawaitana, nati, Mufuna kuti ndikuchitireni chiyani?
33
Ananena kwa Iye, Ambuye, kuti maso athu apenye.
34
Ndipo Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso ao; ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28