bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Matthew 21
Matthew 21
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 22 →
1
Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, kuphiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri,
2
nanena kwa iwo, Mukani kumudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye, masulani iwo, mudze nao kwa Ine.
3
Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asowa iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza.
4
Ndipo ichi chinatero, kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri kuti,
5
Tauzani mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona, mfumu yako idza kwa iwe, wofatsa ndi wokwera pa bulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.
6
Ndipo ophunzirawo anamuka, nachita monga Yesu anawauza;
7
nabwera ndi bulu ndi mwana wake, naika pa iwo zovala zao, nakhala Iye pamenepo.
8
Ndipo ambirimbiri a mpingowo anayala zovala zao panjira; ndipo ena anadula nthambi za mitengo, naziyala m'njiramo.
9
Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana m'Kumwambamwamba!
10
Ndipo m'mene adalowa m'Yerusalemu mudzi wonse unasokonezeka, nanena, Ndani uyu?
11
Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.
12
Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;
13
nanena kwa iwo, Chalembedwa, Nyumba yanga idzanenedwa nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.
14
Ndipo anadza kwa Iye ku Kachisiko akhungu ndi opunduka miyendo, nachiritsidwa.
15
Koma ansembe aakulu ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,
16
nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenga kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?
17
Ndipo Iye anawasiya, natuluka m'mzinda, napita ku Betaniya, nagona kumeneko.
18
Ndipo mamawa, m'mene Iye analinkunkanso kumzinda, anamva njala.
19
Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso kunthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota.
20
Ndipo ophunzira poona ichi anazizwa, nati, Mkuyuwo unafota bwanji msanga?
21
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa.
22
Ndipo zinthu zilizonse mukazifunsa m'kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira.
23
Ndipo m'mene Iye analowa m'Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?
24
Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati mundiuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi:
25
Ubatizo wa Yohane, uchokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu? Koma iwo anafunsana wina ndi mnzake, kuti, Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye?
26
Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.
27
Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, Inenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi.
28
Nanga mutani? Munthu anali nao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito kumunda wampesa.
29
Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pake analapa mtima napita.
30
Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anavomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapite.
31
Ndani wa awiriwo anachita chifuniro cha atate wake? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.
32
Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya chilungamo, ndipo simunamvera iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munachiona, simunalapa pambuyo pake, kuti mumvere iye.
33
Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wamphesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.
34
Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ake kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zake.
35
Ndipo olimawo anatenga akapolo ake, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala.
36
Anatumizanso akapolo ena, akuchuluka oposa akuyambawa; ndipo anawachitira iwo momwemo.
37
Koma pambuyo pake anatumiza kwa iwo mwana wake, nati, Adzachitira mwana wanga ulemu.
38
Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake.
39
Ndipo anamtenga iye, namponya kunja kwa munda, namupha.
40
Tsono atabwera mwini munda, adzachitira olimawo chiyani?
41
Iwo ananena kwa Iye, Adzaononga koipa oipawo, nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zake.
42
Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenga konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?
43
Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.
44
Ndipo iye wakugwa pa mwala uwu adzaphwanyika; koma pa iye amene udzamgwera, udzampera iye.
45
Ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi, pakumva mafanizo ake, anazindikira kuti alikunena za iwo.
46
Ndipo pamene anafuna kumgwira, anaopa makamu a anthu, chifukwa anamuyesa mneneri.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28