bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Matthew 24
Matthew 24
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 25 →
1
Ndipo Yesu anatuluka ku Kachisi; ndipo ophunzira ake anadza kudzamuonetsa chimangidwe cha Kachisiyo.
2
Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa.
3
Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?
4
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu.
5
Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.
6
Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike.
7
Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m'malo akutiakuti.
8
Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.
9
Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.
10
Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake.
11
Ndipo aneneri onama ambiri adzauka, nadzasokeretsa anthu ambiri.
12
Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa kusaweruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazilala.
13
Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.
14
Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.
15
Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)
16
pomwepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri:
17
iye ali pamwamba pa chindwi, asatsikire kunyamula za m'nyumba mwake;
18
ndi iye wa m'munda asabwere kutenga chofunda chake.
19
Koma tsoka ali nalo iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana m'masiku awo!
20
Ndipo pempherani kuti kuthawa kwanu kusakhale pa nyengo yachisanu, kapena pa Sabata;
21
pakuti pomwepo padzakhala masauko akulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.
22
Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.
23
Pomwepo munthu akanena kwa inu, Onani, Khristu ali kuno, kapena uko musamvomereze;
24
chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.
25
Chifukwa chake akanena kwa inu, Onani, Iye ali m'chipululu; musamukeko.
26
Onani, ali m'zipinda; musavomereze.
27
Pakuti monga mphezi idzera kum'mawa, nionekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.
28
Kumene kulikonse uli mtembo, miimba idzasonkhanira konko.
29
Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:
30
ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.
31
Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.
32
Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene tsopano nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira;
33
chomwechonso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti Iye ali pafupi, inde pakhomo.
34
Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.
35
Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai.
36
Koma za tsiku ili ndi nthawi yake sadziwa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.
37
Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.
38
Pakuti monga m'masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'chingalawa,
39
Ndipo iwo sanadziwe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.
40
Pomwepo adzakhala awiri m'munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa:
41
awiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.
42
Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.
43
Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe.
44
Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthawi m'mene simuganizira, Mwana wa Munthu adzadza.
45
Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?
46
Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero.
47
Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang'anira zinthu zake zonse.
48
Koma kapolo woipa akanena mumtima mwake, Mbuye wanga wachedwa;
49
nadzayamba kupanda akapolo anzake, nadya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera;
50
mbuye wa kapoloyo adzafika tsiku losamuyembekeza iye, ndi nthawi yosadziwa iye,
51
nadzamdula, nadzaika pokhala pake ndi anthu onyenga; pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28