bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 John 1
1 John 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 2 →
1
Tikukulemberani za Iye uja amene adaalipo kuyambira pa chiyambi, amene tidamumva ndipo tidamuwona ndi maso athu, amene tidampenya ndithu, ndipo tidamkhudza ndi manja athu: Iyeyo ndiye Mau opatsa moyo.
2
Moyowo udaoneka, ndipo ife tidauwona. Tikuuchitira umboni, ndipo tikukulalikirani za moyo wosatha, umene unali kwa Atate ndipo udatiwonekera.
3
Chimene tidachiwona ndi kuchimva, tikukulalikirani, kuti inunso mukhale a mtima umodzi ndi ife. Kuyanjana kwathu tikuyanjana ndi Atate, ndiponso ndi Mwana wao, Yesu Khristu.
4
Tikukulemberani zimenezi kuti chimwemwe chathu chikhale chathunthu.
5
Uthenga umene tidamva kwa Iye, ndipo timaulalika kwa inu, ndi wakuti Mulungu ndiye kuŵala, ndipo mwa Iye mulibe mdima konse.
6
Tikanena kuti timayanjana naye, pamene tikuyendabe mu mdima, tikunama, ndipo zochita zathu nzosagwirizana ndi zoona.
7
Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
8
Tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga, ndipo mwa ife mulibe choona.
9
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
10
Tikanena kuti sitidachimwe, tikumuyesa wonama Mulungu, ndipo mau ake sali mwa ife.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5