bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 John 2
1 John 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 3 →
1
Inu ana anga, ndikukulemberani zimenezi kuti musamachimwa. Komabe wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, ndiye Yesu Khristu amene ali wolungama.
2
Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi.
3
Pakutsata malamulo a Mulungu, ndi pamene tingatsimikize kuti timamdziŵa.
4
Munthu akamati, “Ine ndimadziŵa Mulungu”, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona.
5
Koma munthu akamasunga mau a Mulungu, pamenepo chikondi cha Mulungu chafikadi pake penipeni mwa iyeyo. Chotitsimikizitsa kuti tili mwa Iye, ndi chimenechi.
6
Munthu akamati amakhala mwa Mulungu, zochita zake zizilingana ndi zimene Yesu ankachita.
7
Inu okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano, koma lakale lomwe lija, limene mwakhala nalo kuyambira pa chiyambi. Lamulo lakalelo ndi mau amene mudaŵamva kale.
8
Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Zimene lamuloli likunena, zidachitikadi mwa Yesu, ndipo zikuchitikanso mwa inu. Pajatu mdima ulikutha, ndipo kuŵala kwenikweni kwayamba kale kuti ngwee.
9
Munthu akamati ali m'kuŵala, komabe nkumadana ndi mnzake, akali mu mdima ameneyo.
10
Koma munthu wokonda mnzake, amakhala m'kuŵala, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa.
11
Munthu wodana ndi mnzake, ali mu mdima, ndipo akuyenda mu mdima. Sadziŵa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa m'maso.
12
Inu ana, ndikukulemberani popeza kuti Mulungu wakukhululukirani machimo anu chifukwa cha dzina la Khristu.
13
Inu atate, ndikukulemberani, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Inu achinyamata, ndikukulemberani, chifukwa mwampambana Woipa uja.
14
Ndimakulemberani inu ana, chifukwa Atate mumaŵadziŵa. Ndimakulemberani inu atate, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Ndimakulemberani inu achinyamata, chifukwa ndinu amphamvu, mau a Mulungu amakhala mwa inu, ndipo mwampambana Woipa uja.
15
Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye.
16
Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.
17
Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
18
Ananu, ino ndi nthaŵi yotsiriza. Mudamva kuti kukubwera Woukira Khristu, ndipo tsopano aoneka kale ambiri oukira Khristu. Zimenezi zikutizindikiritsa kuti ino ndi nthaŵi yotsirizadi.
19
Anthuwo adachita kuchoka pakati pathu, komabe sanali a gulu lathu kwenikweni. Pakuti akadakhala a gulu lathu, bwenzi akali nafebe. Koma adatichokera, kuti aonekere poyera kuti panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene anali wa gulu lathu.
20
Koma inuyo, mudadzozedwa ndi Woyera uja, ndipo nonse mukudziŵa.
21
Ndakulemberani, osati chifukwa chakuti simudziŵa choona, koma chifukwa chakuti mumachidziŵa, ndipo mukudziŵanso kuti bodza silichokera ku choona.
22
Wabodzayo ndani? Kodi si amene amanena kuti Yesu si Mpulumutsi wolonjezedwa uja? Wokana Atate ndi Mwana, ameneyo ndiye Woukira Khristu.
23
Aliyense wokana Mwana, alibenso Atate. Wovomereza Mwana, alinso ndi Atate.
24
Koma inu, zimene mudamva kuyambira pa chiyambi, zikhalebe m'mitima mwanu. Zimene mudamva kuyambira pa chiyambi zikakhalabe m'mitima mwanu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndi mwa Atate.
25
Ndipo chimene adalonjeza nchimenechi: moyo wosatha.
26
Ndikukulemberani zimenezi kuti ndikuuzeni za iwo aja amene amafuna kukusokeretsani.
27
Koma inu, Khristu adakudzozani ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa inu, ndipo sipafunikanso wina woti akuphunzitseni. Mzimu Woyerayo, amene mudadzozedwa naye, amakuphunzitsani zonse. Zimene amakuphunzitsani nzoona, si zonama ai. Nchifukwa chake, monga momwe adakuphunzitsirani, khalani mwa Khristu.
28
Tsono ananu, khalani mwa Iye, kuti tikakhale olimba mtima Iye akadzaoneka, ndipo tisadzachite manyazi Iye akadzabweranso.
29
Ngati mukudziŵa kuti Khristu ndi wolungama, musapeneke konse kuti aliyense wochita chilungamo, ndi mwana wa Mulungu.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5