bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 John 5
1 John 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
1
Munthu aliyense wokhulupirira kuti Yesu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, iyeyo ndi mwana wa Mulungu. Ndipo aliyense wokonda nakubala, amakonda ndi mwana wake yemwe.
2
Chodziŵira kuti timakonda ana a Mulungu nchakuti timakonda Mulungu ndi kutsata malamulo ake.
3
Paja kukonda Mulungu ndiye kuti kutsata malamulo ake, ndipo malamulo ake si olemetsa.
4
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu.
5
Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Amaligonjetsa si wina ai, koma wokhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.
6
Yesu Khristu ndiye amene adabwera kudzera mwa madzi ndi mwa magazi. Sadabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi mwa magazi omwe. Ndipo Mzimu Woyera ndiye amene amachitirapo umboni, pakuti Mzimuyo ndiye choona.
7
Motero pali atatu aŵa ochitira umboni:
8
Mzimu Woyera, madzi ndi magazi, ndipo atatuŵa amavomerezana.
9
Timalandira umboni wa anthu, koma umboni wa Mulungu ndi wopambana umboni wa anthu. Umboniwo ndi umene Mulungu adachitira Mwana wake.
10
Amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu, ali nawo umboniwo mumtima mwake. Amene sakhulupirira Mulungu, amayesa kuti Mulungu ndi wonama, chifukwa sakhulupirira umboni umene Mulungu adachitira Mwana wake.
11
Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake.
12
Amene ali ndi Mwanayo, ali nawo moyo. Amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo.
13
Inu amene mumakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu, ndakulemberani zimenezi kuti mudziŵe kuti muli ndi moyo wosatha.
14
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
15
Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
16
Wina akaona mbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere, ndipo Mulungu adzampatsa moyo mbale wakeyo. Ndikunenatu za ochita tchimo losadzetsa imfa. Koma lilipo tchimo lina lodzetsa imfa, za tchimo limenelo sindikunena kuti apemphere ai.
17
Chinthu chilichonse chosalungama ndi tchimo, koma pali lina tchimo losadzetsa imfa.
18
Tikudziŵa kuti aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamsunga, ndipo Woipa uja sangamkhudze.
19
Tikudziŵa kuti ndife ake a Mulungu, ndipo kuti onse odalira zapansipano ali m'manja mwa Woipa uja.
20
Tikudziŵa kuti Mwana wa Mulungu adafika, ndipo adatipatsa nzeru kuti timdziŵe Mulungu woona. Ndipo tili mwa Mulungu woonayo, chifukwa tili mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona ndiponso moyo wosatha.
21
Ana inu, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
All chapters:
1
2
3
4
5