bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Peter 2
1 Peter 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 3 →
1
Nchifukwa chake tayani choipa chonse, kunyenga konse, chiphamaso, kaduka ndi masinjiriro onse.
2
Monga makanda obadwa chatsopano amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wodyetsa mtima wanu, kuti ukukuzeni ndi kukufikitsani ku chipulumutso,
3
popeza kuti mwachilaŵadi chifundo cha Ambuye.
4
Bwerani kwa Iye amene ali mwala wamoyo womwe anthu adaukana, koma Mulungu adausankha kuti ngwamtengowapatali.
5
Inunso mukhale ngati miyala yamoyo yoti Mulungu amangire nyumba yake. M'menemo muzitumikira ngati ansembe opatulika, pakupereka nsembe zochokera ku mtima, zokomera Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.
6
Paja m'Malembo mudalembedwa kuti. “Ndasankha mwala wamtengowapatali. Ndikuuika tsopano m'Ziyoni, ngati mwala wapangodya. Wokhulupirira Iye sadzachita manyazi.”
7
Tsono kwa inu okhulupirira, Iye ndi wamtengowapatali. Koma kwa osakhulupirira, ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Mwala womwe amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.”
8
Mau a Mulungu akutinso, “Umenewu ndi mwala wokhumudwitsa anthu, ndi thanthwe loŵagwetsa.” Amakhumudwa popeza kuti amakana kumvera mau a Mulungu, ndipo anali oyeneradi kuti adzaone zotere.
9
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
10
Kale simunali anthu a Mulungu, koma tsopano ndinu anthu ake. Kale simudaalandira chifundo, koma tsopano mwachilandira.
11
Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu.
12
Samalani mayendedwe anu pakati pa akunja, kuti ngakhale azikusinjirirani kuti ndinu anthu ochita zoipa, komabe aziwona ntchito zanu zabwino. Apo adzalemekeza Mulungu pa tsiku limene Iye adzaŵayendere.
13
Chifukwa cha Ambuye, muzimvera akulu onse olandira ulamuliro. Ngati ndi mfumu yaikulu koposa ija, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro pa mafumu ena onse.
14
Ngati ndi nduna, zimvereni chifukwa zidachita kutumidwa ndi mfumu kuti zizilanga ochita zoipa ndi kuyamikira ochita zabwino.
15
Paja Mulungu amafuna kuti ndi zochita zanu zabwino muthetse kulankhula kosadziŵa kwa anthu opusa.
16
Inde muzikhala ngati mfulu, koma ufulu wanuwo usakhale ngati chinthu chophimbira zoipa. Koma khalani ngati atumiki a Mulungu.
17
Muzilemekeza anthu onse. Muzikonda akhristu anzanu. Khalani anthu oopa Mulungu. Mfumu yaikulu koposa ija muziipatsa ulemu.
18
Inu antchito, muzimvera ndi ulemu wonse anthu okulembani ntchito, osati okhawo amene ali abwino ndi ofatsa ai, koma ndi ovuta omwe.
19
Pajatu ndi chinthu chabwino ngati munthu, chifukwa chokumbukira Mulungu, apirira zoŵaŵa zosamuyenera.
20
Kodi pali chiyani choti nkukuyamikirani ngati mupirira pamene akumenyani chifukwa choti mwachimwa? Koma mukapirira zoŵaŵa mutachita zabwino, apo mwachita chinthu chovomerezedwa ndi Mulungu.
21
Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zoŵaŵa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake.
22
Iye sadachitepo tchimo lililonse, ndipo sadanene bodza lililonse.
23
Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sadabwezere chipongwe. Pamene ankazunzika, Iye sadaopseze, koma adapereka zonse kwa Mulungu amene amaweruza molungama.
24
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
25
Munali ngati nkhosa zosokera, koma tsopano mwabwerera kwa Mbusa amene ndi wokuyang'anirani.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
Recommended Reading
Commentary
1 Peter Commentaries
→
Devotional
1 Peter Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→