bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Peter 3
1 Peter 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 4 →
1
Chimodzimodzinso inu azimai, muzimvera amuna anu, kuti ngati ena mwa iwo samvera mau a Mulungu, azikopeka ndi makhalidwe a akazi aonu. Sipadzafunikanso kunenerera mau,
2
popeza kuti adzadziwonera okha makhalidwe anu aulemu ndi angwiro.
3
Kudzikongoletsa kwanu kusangokhala kwa maonekedwe akunja pakuluka tsitsi, ndi kuvala zamakaka zagolide ndi zovala zamtengowapatali.
4
Koma kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wam'kati, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengowapatali pamaso pa Mulungu.
5
Umu ndi m'mene kale lija azimai oyera mtima okhulupirira Mulungu ankadzikongoletsera, ndipo ankamvera amuna ao.
6
Sara yemwe ankamvera Abrahamu, ndi kumutcha “Mbuyanga.” Motero inu azimai, ndinu ana ake a Sarayo, ngati muchita bwino, osalola kuwopsedwa ndi kanthu kalikonse.
7
Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.
8
Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.
9
Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.
10
Paja mau a Mulungu akuti. “Yemwe afuna kukondwera ndi moyo, ndi kuwona masiku abwino, aletse lilime lake kulankhula zoipa, ndiponso milomo yake kunena mabodza.
11
Alewe zoipa, azichita zabwino. Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuupeza.
12
Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”
13
Ndani angakuchiteni choipa ngati muchita changu pa zabwino?
14
Koma ngakhale mumve zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo, mudzakhala odala ndithu. Musachite mantha ndi anthu, kapena kuvutika mu mtima,
15
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
16
Khalani ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, kotero kuti anthu ena akamasinjirira mayendedwe anu abwino pamene mukutsata Khristu, achite manyazi ndi chipongwe chao.
17
Nkwabwino kumva zoŵaŵa chifukwa chochita zabwino, ngati Mulungu wafuna choncho, koposa kumva zoŵaŵa chifukwa chochita zoipa.
18
Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.
19
Ndipo ali ngati mzimu choncho, adapita kukalalika kwa mizimu imene inali m'ndende.
20
Mizimuyi ndi ya anthu amene kale lija sadamvere pamene Mulungu adaadikira moleza mtima, pa nthaŵi imene Nowa ankapanga chombo. M'chombomo anthu oŵerengeka okha, asanu ndi atatu, adapulumuka ndi madzi.
21
Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu. Kubatizidwa kumeneku si kuchotsedwa litsiro la m'thupi, koma kudzipereka kwa Mulungu ndi mtima woona, kudzera mwa Yesu Khristu
22
amene adapita Kumwamba, ndipo ali ku dzanja lamanja la Mulungu. Kumeneko angelo ndi maulamuliro ndi zimphamvu zimamvera Iye.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
Recommended Reading
Commentary
1 Peter Commentaries
→
Devotional
1 Peter Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→