bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Peter 4
1 Peter 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 5 →
1
Tsono popeza kuti Khristu adamva zoŵaŵa m'thupi mwake, valani dzilimbe ndi maganizo omwewo, chifukwa munthu amene wamva zoŵaŵa m'thupi mwake, ndiye kuti walekana nawo machimo.
2
Choncho, pa nthaŵi yatsala yoti mukhale pansi pano, simudzatsatanso zilakolako za anthu, koma mudzatsata kufuna kwa Mulungu.
3
Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa.
4
Anthu akunja amadabwa tsopano poona kuti mwaleka kuthamangira nao zoipitsitsa zimene iwo amachita mosadziletsa konse. Nchifukwa chake amalalata.
5
Koma iwo adzayenera kufotokoza okha mlandu wao kwa Mulungu amene ali wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.
6
Nchifukwa chake Uthenga Wabwino udalalikidwa ndi kwa amene adafa omwe, kuti ngakhale adaweruzidwa m'thupi monga anthu, komabe mu mzimu akhale ndi moyo monga Mulungu.
7
Chimalizo cha zonse chayandikira. Nchifukwa chake khalani ochenjera ndi odziletsa, kuti muthe kupemphera.
8
Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.
9
Poyenderana, muzisamalirana bwino mosadandaula.
10
Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.
11
Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.
12
Inu okondedwa, musazizwe ndi chimoto cha masautso chimene chakugwerani kuti muyesedwe nacho. Musaganize kuti zimene zakuwonekeranizo nzachilendo.
13
Koma kondwerani popeza kuti mulikumva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, kuti podzaoneka ulemerero wake, mudzasangalale kwakukulu.
14
Anthu akakuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, chifukwa ndiye kuti Mzimu wa ulemerero, Mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu.
15
Pakati panu pasakhale ndi mmodzi yemwe wogwa m'mavuto chifukwa choti wapha munthu, kapena waba, kapena wachita choipa, kapena waloŵerera za eniake.
16
Koma ngati mumva zoŵaŵa chifukwa chakuti ndinu akhristu, musachite manyazi, koma mulemekeze Mulungu chifukwa cha dzinalo.
17
Nthaŵi ndiye yafika yoti Mulungu ayambe kuweruza anthu ake. Tsono ngati chiweruzocho chiyambira pa ife, nanga podzafika pa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, ndiye kuti chidzakhala chotani?
18
Paja mau a Mulungu akuti, “Ngati wolungama yemwe adzapulumuka movutikira, nanga munthu wochimwa, wonyozera za Mulungu, adzatani?”
19
Nchifukwa chake anthu amene amamva zoŵaŵa monga Mulungu afunira, adzipereke m'manja mwa Mlengi wao wokhulupirika, ndi kumachitabe ntchito zabwino.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
Recommended Reading
Commentary
1 Peter Commentaries
→
Devotional
1 Peter Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→