bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Thessalonians 3
1 Thessalonians 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 4 →
1
Nchifukwa chake pamene sitidathenso kupirira, tidalolera kutsalira tokha ku Atene.
2
Choncho tidatuma Timoteo, mbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yolalika Uthenga Wabwino wa Khristu. Tidamtuma kuti adzakulimbitseni mtima ndi kukukhazikitsani m'chikhulupiriro chanu,
3
kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angagwedezeke chifukwa cha mazunzoŵa. Mukudziŵa nokha kuti Mulungu ndiye adalola kuti zimenezi zitigwere.
4
Pajatu pamene tinali pamodzi nanu, tidaakuuziranitu kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziŵa, zimenezi zidachitikadi.
5
Nchifukwa chake, pamene sindidathenso kupirira, ndidatuma Timoteo kuti adzaone m'mene chiliri chikhulupiriro chanu. Pakuti ndinkaopa kuti kapena Satana, Wonyenga uja, adakunyengani, ndipo kuti ntchito zathu zonse pakati panupo zidangopita pachabe.
6
Koma tsopano Timoteo wabwerako kuchokera kwanuko, ndipo watisimbira mbiri yokoma ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumalakalaka kutiwona ife, monga momwe ifeyo timafunitsitsira kukuwonaninso inuyo.
7
Motero abale, pakati pa masautso ndi mazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatithuzitsa mtima.
8
Takhalanso ndi moyo tsopano pakuti mukulimbika pa chikhristu chanu.
9
Nanga tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira chifukwa cha inu, poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu?
10
Ndi mtima wonse timapemphera usana ndi usiku kuti tiwonane nanunso maso ndi maso, kuti tikakwaniritse zimene zikusoŵa pakuwonetsa chikhulupiriro chanu.
11
Tikupempha kuti Mulungu Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko.
12
Ambuye akulitsirekulitsire kukondana kwanu, ndiponso chikondi chanu cha pa anthu onse, monga momwe chikondi chathu cha pa inu chikukulirakulira.
13
Motero Iye adzalimbitsa mitima yanu kuti idzakhale yangwiro ndi yoyera pamaso pa Mulungu Atate athu, pamene Ambuye Yesu adzabwerenso pamodzi ndi oyera ake onse.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5