bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Thessalonians 5
1 Thessalonians 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
1
Komatu abale, za nthaŵi ndi nyengo yake yodzachitika zimenezi, nkosafunikira kuti ndichite kukulemberani.
2
Inu nomwe mukudziŵa bwino kuti tsiku la Ambuye likadzafika ngati mbala yausiku.
3
Pamene anthu azikati, “Pali mtendere, tili pabwino”, pamenepo chiwonongeko chidzaŵagwera modzidzimutsa. Chidzaŵadzidzimutsa monga momwe zoŵaŵa zimamchitira mkazi pa nthaŵi yoti achire; ndipo sadzatha konse kuchizemba.
4
Koma inu abale, simuli m'chimbulimbuli kuti tsikulo nkukudzidzimutsani ngati mbala.
5
Paja nonsenu zanu zonse ndi zam'kuŵala, ndiye kuti zausana. Ife zathu si zausiku kapena zamumdima ai.
6
Nchifukwa chake tsono tisagone tulo monga momwe amachitira anthu ena, ife tikhale maso, tikhale osaledzera.
7
Anthu ogona tulo, amagona usiku, anthu oledzera amaledzera usiku.
8
Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka.
9
Paja Mulungu sadatisankhe kuti tidzaone mkwiyo wake, koma kuti tidzalandire chipulumutso kwa Ambuye athu Yesu Khristu.
10
Iwo adatifera kuti tikakhale ndi moyo pamodzi naye, ngakhale pamene tili amoyo kapena titafa kale.
11
Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.
12
Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani.
13
Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.
14
Abale, tikukupemphani kuti anthu amene amangokhala osafuna kugwira ntchito muziŵadzudzula, anthu otaya mtima muziŵalimbikitsa. Anthu ofooka muziŵathandiza, anthu onsewo muziŵalezera mtima.
15
Onetsetsani kuti wina aliyense mnzake akamchita choipa, asabwezere choipacho. Koma nthaŵi zonse muziyesetsa kuchitira zabwino anzanu ndi anthu ena onse.
16
Khalani okondwa nthaŵi zonse.
17
Muzipemphera kosalekeza.
18
Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
19
Musayese kuletsa ntchito ya Mzimu Woyera.
20
Musanyoze mau olalikidwa m'dzina la Mulungu,
21
koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino,
22
ndipo mupewe choipa cha mtundu uliwonse.
23
Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu.
24
Iye amene akukuitanani ngwokhulupirika, ndipo adzakuchitirani zimenezi.
25
Abale, muzitipempherera.
26
Abale onse muŵapatseko moni mwachikondi.
27
M'dzina la Ambuye ndikukulamulani kuti kalatayi muŵaŵerengere abale onse.
28
Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
All chapters:
1
2
3
4
5