bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Thessalonians 4
1 Thessalonians 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 5 →
1
Potsiriza tsono, abale, tifuna tikupempheni kanthu. Mudalandira kwa ife mau onena za m'mene muziyendera kuti mukondweretse Mulungu. Mukutsata mayendedwe otere kumene, koma tikukupemphani kolimba m'dzina la Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale.
2
Pakuti mukudziŵa malangizo amene tidakupatsani ochokera kwa Ambuye Yesu.
3
Chimene Mulungu akufuna ndi ichi: mukhale oyera mtima, ndiye kuti muzipewa dama.
4
Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa.
5
Musamangotsata zilakolako zonyansa, monga amachitira akunja, amene sadziŵa Mulungu.
6
Pa zimenezi munthu asachimwire mbale wake kapena kumpezera. Monga tidakuuzani kale monenetsa, Ambuye adzalanga anthu onse ochita zotere.
7
Paja Mulungu sadatiitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima.
8
Motero munthu wokana mau ameneŵa, sakukana munthu chabe ai, koma akukana Mulungu amene amakupatsani Mzimu wake Woyera.
9
Kunena za kukondana pakati pa akhristu, nkosafunikira kuti ndichite kukulemberani, popeza kuti ndi Mulungu mwini amene adakuphunzitsani za m'mene muyenera kukonderana.
10
Ndipo mumakondana nawodi abale onse a m'dziko lonse la Masedoniya. Koma tikukupemphani abale, kuti muchite zimenezi koposa kale.
11
Yesetsani kukhala ndi moyo wabata. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kumagwira ntchito ndi manja ake. Chitani zimenezi, monga tidakulangizirani muja,
12
kuti akunja azikulemekezani, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.
13
Abale, tifuna kuti mudziŵeko za anthu amene adamwalira, kuti chisoni chanu chisakhale ngati cha anthu ena amene alibe chiyembekezo.
14
Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.
15
Tsopano tikuuzeni mau a Ambuye mwini. Ife amoyofe, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sikuti tidzaŵasiya kumbuyo amene adamwalira aja ai.
16
Padzakhala mfuu wa mau a mngelo wamkulu ndi wa lipenga la Mulungu. Ndipo pamenepo Ambuye mwini adzatsika kuchokera Kumwamba. Anthu amene adafa akukhulupirira Khristu, adzayamba ndiwo kuuka.
17
Pambuyo pake ife amoyofe, otsalafe, tidzatengedwa pamodzi nawo m'mitambo kuti tikakumane ndi Ambuye mu mlengalenga. Motero tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse.
18
Nchifukwa chake tsono muzithuzitsana mtima pokambirana zimenezi.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5