bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Timothy 2
1 Timothy 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 3 →
1
Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu.
2
Muziŵapempherera mafumu ndi onse amene ali ndi ulamuliro, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, tizitamanda Mulungu pa zonse ndi kumadzilemekeza.
3
Zimenezi nzabwino ndi zokondweretsa pamaso pa Mulungu, Mpulumutsi wathu.
4
Iye amafuna kuti anthu onse apulumuke ndipo kuti adziŵe choona.
5
Pajatu Mulungu ndi mmodzi yekha, Mkhalapakati mmodzi yekhanso pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja timati Khristu Yesu.
6
Iyeyo adadzipereka kuti akhale momboli wa anthu onse. Umenewu unali umboni umene udaperekedwa pa nthaŵi yake.
7
Nchifukwa chake ine adandiika kuti ndikhale mlaliki wake ndiponso mtumwi, wophunzitsa anthu a mitundu ina mau a chikhulupiriro choona. Sindikunamatu ai, ndikunena zoona.
8
Ndikufuna kuti paliponse amuna popemphera azikweza manja ao kwa Mulungu momchitira ulemu, mopanda mkwiyo kapena kukangana.
9
Ndikufunanso kuti akazi azivala mwaulemu, mwanzeru ndi moyenera. Inde adzikongoletse, komatu osati ndi tsitsi lochita kukonza monyanyira, kapena ndi zokongoletsa zagolide, kapena mikanda yamtengowapatali, kapena zovala zamtengowapatali.
10
Kwenikweni adzikongoletse ndi ntchito zabwino, monga ayenera kuchitira akazi amene amati ndi opembedza Mulungu.
11
Akazi pophunzitsidwa, azikhala chete ndi a mtima wodzichepetsa.
12
Sindilola kuti mkazi aziphunzitsa kapena kukhala ndi ulamuliro pa amuna. Mkazi kwake nkukhala chete.
13
Paja Adamu ndiye adaayambira kulengedwa, pambuyo pake Heva.
14
Ndiponso si Adamu amene adaanyengedwa, koma mkaziyo ndiye adaanyengedwa, naphwanya lamulo la Mulungu.
15
Koma mkazi adzapulumukabe kudzera m'kubala ana, malinga akalimbikira modzichepetsa m'chikhulupiriro, m'chikondi ndi m'kuyera mtima.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6