bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Timothy 5
1 Timothy 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 6 →
1
Munthu wachikulire usamdzudzule mokalipa, koma umchenjeze monga ngati bambo wako. Amuna achinyamata uzikhalitsana nawo ngati abale ako.
2
Azimai achikulire uzikhalitsana nawo ngati amai ako, ndipo azimai a zaka zochepa uzikhalitsana nawo ngati alongo ako, m'kuyera mtima kwenikweni.
3
Uziŵachitira ulemu azimai amasiye, amenetu ali amasiye enieni.
4
Koma ngati mai wamasiye ali ndi ana kapena adzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wao pa banja lao moopa Mulungu, kuti pakutero abwezere makolo ao zimene adalandira kwa iwo. Pakuti zimenezi Mulungu amakondwera nazo akamaziwona.
5
Mai amene ali wamasiye kwenikweni, wopanda wina aliyense womsamala, ameneyo waika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimthandiza.
6
Koma mai wamasiye amene amangodzisangalatsa ndi zapansipano, ameneyo wafa kale ngakhale akali moyo.
7
Uziŵalamula zimenezi, kuti akhale opanda mlandu.
8
Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.
9
Wina aliyense asaloledwe kuloŵa m'gulu la azimai amasiye, asanakwanitse zaka 60. Akhale woti adakwatiwapo ndi mwamuna mmodzi yekha.
10
Akhale mai woti anthu amamchitira umboni wakuti amachitadi ntchito zabwino. Akhale woti ankalera ana ake bwino, ankalandira bwino alendo, ankasambitsa mapazi a anthu a Mulungu, ndipo ankathandiza anthu amene anali m'mavuto. Akhalenso mai woti ankadzipereka pa ntchito zonse zabwino.
11
Koma azimai amasiye a zaka zochepera uzikana kuŵalemba m'gulu limeneli. Pajatu zilakolako zao zikayamba kuŵavutitsa nkuŵalekanitsa ndi Khristu, amangofuna kukwatiwanso.
12
Pamenepo amapezeka olakwa, chifukwa chosasunga lonjezo lao loyamba.
13
Kuwonjezera pamenepo, amagwa m'chizoloŵezi cha kungokhala khale, motero amangoyendayenda ku nyumba za anthu. Tsonotu samangokhala khale chabe ai, amachitanso miseche nkumaloŵera za eni, ndi kukhala omalankhula zimene samayenera kulankhula.
14
Nchifukwa chake nkadakonda kuti azimai amasiye a zaka zochepera azikwatiwanso, abale ana, ndipo azisamala bwino panyumba pao, kuti adani athu asapeze mpata wotisinjirira.
15
Paja alipo kale azimai amasiye ena amene adapatukapo nkumatsata Satana.
16
Koma ngati mai wina aliyense wachikhristu ali ndi achibale amene ali azimai amasiye, aziŵasamala iyeyo, osasenzetsa mpingo katundu wakeyo. Motero mpingo udzatha kusamala azimai amasiye opanda oŵathandiza.
17
Akulu a mpingo otsogolera mpingo bwino, akhale oyenera kuŵalemekeza moŵirikiza, makamaka amene amagwira ntchito yolalika mau a Mulungu ndiponso yophunzitsa.
18
Paja Malembo akuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe imene ikupuntha tirigu.” Penanso akuti, “Wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake.”
19
Usamamvere mau oneneza mkulu wa mpingo, pokhapokha ngati pali mboni ziŵiri kapena zitatu.
20
Opitirirabe kuchimwa uziŵadzudzula pamaso pa onse, kuti ena onsewo achite mantha.
21
Pamaso pa Mulungu, pamaso pa Khristu Yesu, ndi pamaso pa angelo onse osankhidwa, ndikukulamula ndithu kuti uzitsata malamulo ameneŵa mopanda tsankho, ndipo kuti usachite chilichonse mokondera.
22
Usafulumire kumsanjika manja munthu, ndipo usavomerezane ndi anthu ena pa uchimo wao. Iwe usunge bwino kuyera mtima kwako.
23
Uleke kumangomwa madzi okha. Koma uzimwako vinyo pang'ono, paja umavutika ndi m'mimba, ndiponso chifukwa cha kudwaladwala kwako kuja.
24
Pali anthu ena amene machimo ao amaonekeratu poyera asanakambe nkomwe mlandu wao, m'menemo ena machimo ao amayamba kudziŵika pokamba mlandu.
25
Momwemonso ntchito zokoma zimaonekera poyera, ndipo ngakhale zipande kutero, sizingathe kubisika nthaŵi zonse.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6