bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
1 Timothy 4
1 Timothy 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 5 →
1
Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.
2
Zophunzitsa zimenezi nzochokera ku chinyengo cha anthu onama, amene mumtima mwao adalembedwa chizindikiro ndi chitsulo chamoto.
3
Iwo amaletsa anthu ukwati, nkumaŵalamula kusala zakudya zina. Koma tsono zakudyazo Mulungu adazilenga kuti amene ali okhulupirira ndi odziŵa choona, azidye moyamika Mulungu.
4
Pajatu chilichonse chimene Mulungu adalenga nchabwino, palibe chilichonse choti munthu asale, akamachilandira moyamika Mulungu,
5
pakuti chimayeretsedwa ndi mau a Mulungu ndi mapemphero aja.
6
Ngati abale uŵalangiza zimenezi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa ndi mau a chikhulupiriro ndi a chiphunzitso choona chimene wakhala ukutsata.
7
Koma upewe nthano zachabe, monga zimene akazi okalamba amakonda kukamba. Udzizoloŵeze kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu.
8
Kuzoloŵeza thupi kumapindulitsapo pang'ono, koma moyo wolemekeza Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo wakutsogolo.
9
Ameneŵa ndi mau otsimikizika oyenera kuŵavomereza ndi mtima wonse.
10
Nchifukwa chake timagwira ntchito kolimba, ndipo timayesetsa kupambana, pakuti chiyembekezo chathu chili pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka okhulupirira Khristu.
11
Uzilamula ndi kuphunzitsa zimenezi.
12
Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.
13
Mpaka pamene ndidzabwere, uchite khama kuŵerengera anthu mau a Mulungu, kuŵalalikira ndi kuŵaphunzitsa.
14
Usanyozere mphatso yaulere ija ili mwa iweyi, imene udailandira kudzera m'mau otchulidwa m'dzina la Mulungu, pamene gulu la akulu a Mpingo lidaakusanjika manja.
15
Ntchito zimenezi uzizichita mosamala ndi modzipereka, kuti anthu onse aone kuti moyo wako wautumiki ukukulirakulira.
16
Udziyang'anire bwino wekha, ndi kusamala zimene umaphunzitsa. Ulimbikire kutero, chifukwa pakuchita zimenezi udzadzipulumutsa iwe wemwe, ndiponso anthu amene amamva mau ako.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6