bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Timothy 2
2 Timothy 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 3 →
1
Tsono iwe, mwana wanga, limbika pakugwiritsa ntchito mphatso zaulere zimene uli nazo mwa Khristu Yesu.
2
Mau amene udamva kwa ine pamaso pa mboni zambiri, uŵasungitse anthu okhulupirika amene adzathe kuŵaphunzitsanso kwa ena.
3
Umve nao zoŵaŵa monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu.
4
Msilikali amene akumenya nkhondo sasamalako ntchito zakumudzi, chifukwa iye amangofuna kukondweretsa mkulu wa ankhondo.
5
Munthu wothamanga pa mpikisano wa liŵiro, sangalandire mphotho ngati sathamanga motsata malamulo a mpikisanowo.
6
Mlimi wogwira ntchitoyo molimbika, ndiye ayenera kukhala woyamba kulandira nao zipatso.
7
Uganizire bwino zimene ndikunenazi, Ambuye adzakuthandiza kumvetsa zonse.
8
Kumbukira Yesu Khristu amene adauka kwa akufa, ndiponso anali mmodzi mwa zidzukulu za Davide, monga umaphunzitsira Uthenga Wabwino umene ine ndimalalika.
9
Chifukwa cha Uthenga Wabwinowu ndimamva zoŵaŵa, mpakanso kumangidwa m'ndende, ngati chigaŵenga. Koma mau a Mulungu sangathe kumangidwa.
10
Motero tsono ndimapirira zonsezi chifukwa cha anthu amene Mulungu adaŵasankha, kuti iwonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu, ndi kulandira ulemerero wamuyaya.
11
Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu: “Ngati tidafa pamodzi naye, tidzakhala moyonso pamodzi naye.
12
Ngati tilimbika, tidzakhala mafumu pamodzi naye. Ngati ife timkana, Iyenso adzatikana.
13
Ngati ndife osakhulupirika, Iye amakhalabe wokhulupirika, pakuti sangathe kudzitsutsa.”
14
Uziŵakumbutsa zimenezi anthu, ndipo uŵachenjeze kolimba pamaso pa Mulungu kuti asamakangana pa za mau. Kutero kulibe phindu, koma kumangotayikitsa anthu amene akumva kukanganako.
15
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.
16
Koma nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, uzipewe, pakuti anthu olankhula zotere adzanka nanyozeranyozera Mulungu.
17
Ndipo zophunzitsa zao zidzaloŵerera mu anthu ngati kunyeka kwa chilonda. Mwa anthu ameneŵa wina ndi Himeneo, wina ndi Fileto.
18
Iwowo adasokera nkusiya choona. Amaphunzitsa kuti kuuka kwa akufa kudachitika kale. Motero amasokoneza chikhulupiriro cha anthu ena.
19
Komabe maziko olimba, amene Mulungu adaŵaika, ngokhazikika, ndipo mau olembedwapo ndi aŵa: “Ambuye amadziŵa amene ali ao”, ndiponso, “Aliyense wotamanda dzina la Ambuye, asiye zosalungama.”
20
M'nyumba yaikulu simukhala ziŵiya zagolide kapena zasiliva zokhazokha; mumakhalanso zamtengo kapena zadothi. Zina zimakhala za ntchito zolemerera, zina za ntchito wamba.
21
Tsono munthu akadziyeretsa nkusiya zotsikazi, adzakhala ngati chiŵiya cha ntchito zolemerera. Adzakhala wopatulika ndi wofunika zedi kwa Ambuye ake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.
22
Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.
23
Uzikana matsutsano opusa ndi opanda nzeru, paja ukudziŵa kuti zotere zimautsa mikangano.
24
Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto.
25
Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona.
26
Pamenepo nzeru zao zidzabweramo, ndipo adzapulumuka mu msampha wa Satana, amene adaaŵagwira kuti azichita zofuna zake.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
Recommended Reading
Commentary
2 Timothy Commentaries
→
Devotional
2 Timothy Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→