bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Timothy 4
2 Timothy 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
1
Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza anthu onse, amoyo ndi akufa omwe, ndipo potamanda kubwera kwake ndi ufumu wake wa Khristuyo ndikukulamula ndithu kuti
2
uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.
3
Paja nthaŵi idzafika pamene anthu azidzakana chiphunzitso choona. M'malo mwake, chifukwa cholakalaka kumva zoŵakomera zokha, adzadzisankhira aphunzitsi ochuluka omaŵauza zimene iwo akufuna.
4
Adzafulatira choona, osafunanso kuchimva, ndipo adzangotsata nthano chabe.
5
Koma iwe, uzikhala maso pa zonse, pirira pa zoŵaŵa, gwira ntchito yolalika Uthenga Wabwino. Kwaniritsa udindo wako mosamala.
6
Paja ine ndiye moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthaŵi yafika kuti ndinyamuke ulendo wanga wochoka m'moyo uno.
7
Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liŵiro, ndasunga chikhulupiriro.
8
Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungira. Ambuye amene ali Woweruza wolungama, ndiwo amene adzandipatsa mphothoyo pa tsiku la chiweruzo. Tsonotu sadzangopatsa ine ndekha ai, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso.
9
Uyesetse kubwera kuno msanga.
10
Paja Dema adandisiya chifukwa chokonda zapansipano, adapita ku Tesalonika. Kresike adapita ku Galatiya, ndipo Tito adapita ku Dalamatiya.
11
Luka yekha ndiye ali ndi ine. Ukatenge Marko udzabwere naye kuno, chifukwa amene uja angathe kundithandiza pa ntchito.
12
Ndidatuma Tikiko ku Efeso.
13
Pobwera unditengereko mwinjiro wanga umene ndidasiya kwa Karpo ku Troasi. Unditengerenso mabuku anga, makamaka aja azikopaŵa.
14
Aleksandro, mmisiri wa zosulasula uja adandichita zoipa kwambiri. Ambuye adzamlanga molingana ndi zimene adachita.
15
Iwenso uchenjere naye, chifukwa iye uja adatsutsa kwamphamvu zolalika ife.
16
Pamene ndinkadziteteza pa mlandu wanga poyamba paja, panalibe ndi mmodzi yemwe amene adabwera kudzandithandiza, onse adangondisiya ndekha. Mulungu aŵakhululukire.
17
Koma Ambuye adakhala nane limodzi, adandilimbitsa mtima kuti ndilalike mau onse a Uthenga Wabwino, kuti anthu a mitundu yonse aŵamve. Motero ndidapulumuka m'kamwa mwa mkango.
18
Ambuye adzandipulumutsanso ku chilichonse chofuna kundichita choipa, ndipo adzandisunga bwino mpaka kundiloŵetsa mu Ufumu wake wa Kumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero kwamuyaya. Amen.
19
Uperekeko moni kwa Prisika ndi Akwila ndiponso kwa a m'banja la Onesifore.
20
Erasito adatsalira ku Korinto, ndipo Trofimo ndidamsiya akudwala ku Mileto.
21
Uyesetse ndithu kubwera isanafike nyengo yachisanu. Yubulo, Pude, Lino, Klaudia, ndi abale ena onse akuti moni.
22
Ambuye akhale nawe. Mulungu akukomereni mtima nonse.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
All chapters:
1
2
3
4
Recommended Reading
Commentary
2 Timothy Commentaries
→
Devotional
2 Timothy Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→