bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Timothy 3
2 Timothy 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
1
Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta.
2
Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu.
3
Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino,
4
opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu.
5
Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.
6
Ena mwa iwo amaloŵa m'nyumba za anthu nkumakanyenga akazi ofooka, olemedwa ndi katundu wa machimo. Akazi ameneŵa amatengeka ndi zilakolako zamitundumitundu,
7
amangomvera za aliyense, ndipo sangathe konse kudziŵa choona.
8
Monga momwe Yane ndi Yambere adaaukira Mose, anthu amenewonso amaukira choona. Nzeru zao nzobuntha, ndipo pa za chikhulupiriro ndi anthu olephera.
9
Koma sadzapitirira nazo, pakuti anthu onse adzaona kupusa kwao, monga momwe zidaachitikiranso ndi Yane uja ndi Yambere.
10
Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga,
11
mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi.
12
Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi,
13
m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe.
14
Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa.
15
Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu.
16
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama.
17
Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
Recommended Reading
Commentary
2 Timothy Commentaries
→
Devotional
2 Timothy Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→