bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Colossians 1
Colossians 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 2 →
1
Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu. Ndili limodzi ndi Timoteo, mbale wathu.
2
Tikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu okhala ku Kolose, abale athu okhulupirika mwa Khristu. Mulungu Atate athu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
3
Tikamakupemphererani, nthaŵi zonse timathokoza Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
4
Timathokoza chifukwa tamva kuti mumakhulupirira Khristu Yesu, ndiponso kuti mumakonda anthu onse a Mulungu.
5
Gwero la zonsezi ndi chiyembekezo chimene muli nacho chodzalandira zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Mudamva za zimenezi pamene mau oona, adakufikani poyamba paja. Mau oonawo ndi Uthenga Wabwino.
6
Uthenga Wabwinowu ukubala zipatso ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi, monga momwe wachitiranso pakati panu, kuyambira tsiku limene mudamva ndi kumvetsa za kukoma mtima kwa Mulungu.
7
Mudaphunzira zimenezi kwa Epafra, mtumiki mnzathu wokondedwa. Iye uja akugwirira ntchito Khristu mokhulupirika m'malo mwathu.
8
Ndiye amene adatidziŵitsa za chikondi chomwe Mzimu Woyera adaika mwa inu.
9
Nchifukwa chake, kuyambira tsiku limene tidamva zimenezi, sitileka kukupemphererani. Timapempha Mulungu kuti akudzazeni ndi nzeru ndi luntha, zimene Mzimu Woyera amapatsa, kuti mumvetse zonse zimene Iye afuna.
10
Pamenepo mudzatha kuyenda m'njira zimene Ambuye amafuna, ndi kuŵakondweretsa pa zonse. Pakugwira ntchito zabwino zamitundumitundu, moyo wanu udzaonetsa zipatso, ndipo mudzanka muwonjezerawonjezera nzeru zanu za kudziŵa Mulungu.
11
Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yaulemerero, kuti muzipirira zonse ndi mitima yoleza ndi yosangalala.
12
Ndipo timapemphera kuti muziyamika Atate, amene adakuyenerezani kuti mudzalandire nao madalitso onse amene amasungira anthu ao mu ufumu wa kuŵala.
13
Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa.
14
Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.
15
Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka. Iye ndiye Mwana wake woyamba, wolamulira zolengedwa zonse.
16
Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo.
17
Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi.
18
Iye ndiyenso mutu wa mpingo thupi lake. Ndiye chiyambi chake, Woyambirira mwa ouka kwa akufa, kuti pa zonse Iye akhale wopambana ndithu.
19
Kudakomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristuyo.
20
Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
21
Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'ntchito zanu zoipa.
22
Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse.
23
Koma tsono muzikhala okhazikika kolimba pa maziko a chikhulupiriro chanu, osasunthika pa chiyembekezo chofumira ku Uthenga Wabwino umene mudamva. Uthenga Wabwinowu walalikidwa kwa anthu a pa dziko lonse lapansi, ndipo Mulungu ndiye adandipatsa ine, Paulo, ntchito yoti ndiwulalike.
24
Tsopano ndakondwa kuti ndikukuvutikirani. Pakuti pakumva zoŵaŵazo, ndikutsiriza m'thupi mwanga zotsala za masautso a Khristu kuthandiza thupi lake, ndiye kuti Mpingo.
25
Ndipo ine ndine mtumiki wa Mpingowu, pakuti Mulungu ndiye adandipatsa ntchitoyi yoti ndikulalikireni kwathunthu mau ake.
26
Mauwo ndi chinsinsi chozama chimene chinali chobisika chikhalire kwa mibadwo yonse, koma tsopano Mulungu wachiwululira anthu ake.
27
Cholinga cha Mulungu ndi cha kudziŵitsa anthuwo kukoma kwake kwa chinsinsicho ndi ulemerero wake pakati pa anthu akunja. Chinsinsicho nchakuti Khristu ali mwa inu, ndipo Iye amakupatsani chiyembekezo cha kudzalandira ulemerero.
28
Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.
29
Ndi cholinga chimenechi ndikugwiradi ntchito kwambiri ndi mphamvu ya Khristu imene ikugwira ntchito kolimba mwa ine.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4