bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Colossians 3
Colossians 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
1
Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu.
2
Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.
3
Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.
4
Khristu ndiye moyo wanu weniweni tsopano, choncho pamene Iye adzaonekerenso, inunso mudzaonekera mu ulemerero pamodzi naye.
5
Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.
6
Chifukwa cha zinthu zotere Mulungu amaŵakwiyira anthu osamumvera.
7
Inunso kale makhalidwe anu anali omwewo, munkachita zomwezo.
8
Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa.
9
Musamauzana mabodza, pakuti mwachita ngati mwavula moyo wanu wakale, pamodzi ndi zochitachita zake zoipa,
10
ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye.
11
M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse.
12
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
13
Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.
14
Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
15
Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.
16
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
17
Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
18
Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye.
19
Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai.
20
Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye.
21
Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, kuti angataye mtima.
22
Inu antchito, muziŵamvera pa zonse ambuye anu apansipano. Musamangochitatu zimenezi pamene muli pamaso pao kuti akuyamikireni, koma muziŵamvera ndi mtima wonse, chifukwa choopa Ambuye.
23
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai.
24
Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.
25
Koma munthu amene amachita zosalungama, zidzamubwerera, chifukwa Mulungu amaweruza mosakondera.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4