bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Colossians 4
Colossians 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
1
Inu ambuye, antchito anu muzikhalitsana nawo mwachilungamo ndi moyenera, podziŵa kuti inunso muli ndi Mbuye wanu Kumwamba.
2
Muzipemphera mosafookera, ndipo pamene mukupemphera, muzikhala tcheru ndiponso oyamika Mulungu.
3
Ifeyonso muzitipempherera kuti Mulungu atipatse mwai woti tilalike mau ake, makamaka kuti tilengeze chinsinsi chozama chokhudza Khristu. Chifukwa cha kulalika chinsinsichi ndine womangidwa m'ndende muno.
4
Mundipempherere tsono kuti ndichifotokoze bwino monga ndiyenera.
5
Mayendedwe anu pakati pa anthu akunja azikhala anzeru, ndipo muzichita changu, osataya nthaŵi pachabe.
6
Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.
7
Tikiko, mbale wathu wokondedwa, adzakudziŵitsani zonse za ine. Iyeyo ndi mtumiki wokhulupirika, wantchito mnzathu pa ntchito ya Ambuye.
8
Nchifukwa chake ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti adzakulimbitseni mtima.
9
Ndikumtuma pamodzi ndi Onesimo, mbale wathu wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali mmodzi mwa inu. Iwo adzakudziŵitsani zonse zakuno.
10
Aristariko, mkaidi mnzanga, akukupatsani moni. Akuteronso Marko, msuweni wa Barnabasi. Za Markoyo mudalandira kale mau akuti akafika kwanuko, mumlandire bwino.
11
Akutinso moni Yesu, wotchedwa Yusto. Mwa ochokera ku Chiyuda ndi atatu okhaŵa amene akundithandiza pa ntchito ya Ufumu wa Mulungu, ndipo andilimbikitsa kwambiri.
12
Akukupatsani moni Epafra, amene ali mmodzi mwa inu, ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu. Nthaŵi zonse iyeyo amalimbikira kukukumbukirani m'mapemphero ake. Amatero pofuna kuti inuyo mukhale okhazikika, angwiro, ndipo kuti muzichilimikira kuchita zonse zimene Mulungu afuna.
13
Ndingathe kumchitira umboni kuti amagwira ntchito kwambiri chifukwa cha inu, ndiponso chifukwa cha anthu okhala ku Laodikea ndi ku Hierapoli.
14
Luka, sing'anga wathu wokondedwa, ndiponso Dema, onsewo akuti moni.
15
Mutiperekereko moni kwa abale athu okhala ku Laodikea, ndiponso kwa Nimfa ndi kwa ampingo amene amasonkhana kunyumba kwake.
16
Kalatayi itaŵerengedwa pakati panu, ikaŵerengedwenso mu mpingo wa ku Laodikea. Ndipo inunso muŵerengeko kalata imene a ku Laodikea adzakutumizirani.
17
Uzani Arkipo kuti, “Samala bwino kuti ntchito imene Ambuye adakupatsa uziigwira moikapo mtima.”
18
Ndi dzanja langalanga ndikulemba mau aŵa: “Moni. Ndine Paulo.” Kumbukirani kuti ndili m'maunyolo. Mulungu akukomereni mtima.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
All chapters:
1
2
3
4