bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Galatians 1
Galatians 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 2 →
1
Ndine, Paulo, mtumwi. Adandisankha si anthu ai, koma Yesu Khristu, ndiponso Mulungu Atate amene adamuukitsa kwa akufa.
2
Ineyo pamodzi ndi abale onse amene ali nane, tikulembera mipingo ya ku Galatiya.
3
Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
4
Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna.
5
Ulemu ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya. Amen.
6
Ndikudabwa kuti mukupatuka msangamsanga motere, kusiya Mulungu amene adakuitanani mwa kukoma mtima kwa Khristu, ndipo kuti mukutsata uthenga wabwino wina.
7
Koma palibe konse uthenga wabwino wina. Pali anthu ena amene akukusokonezani, ndipo akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wonena za Khristu.
8
Koma aliyense, kaya ndife kaya ndi mngelo wochokera Kumwamba, akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi uja tidakulalikiraniwu, ameneyo akhale wotembereredwa.
9
Ndikubwereza kunena zimene tidaanenanso kale, kuti munthu aliyense akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi Uthenga Wabwino umene mudalandira uja, iyeyo akhale wotembereredwa.
10
Kodi ponena zimenezi ndiye kuti ndikufuna kuti anthu andivomereze? Iyai, koma kuti andivomereze ndi Mulungu. Kodi ndikuyesa kukondweretsa anthu? Ndikadayesabe kukondweretsa anthu, si bwenzi ndilinso mtumiki wa Khristu.
11
Abale, ntakuuzani: Uthenga Wabwino umene ine ndimalalika, ndi wosachokera kwa anthu.
12
Sindidaulandire kwa munthu, ndipo palibenso munthu amene adandiphunzitsa Uthengawo, koma ndi Yesu Khristu yemwe amene adawuulula kwa ine.
13
Mudamva za mayendedwe anga kale pamene ndinali m'Chiyuda. Ndinkazunza Mpingo wa Mulungu koopsa, ndipo ndinkayesetsa kuuwonongeratu.
14
Ndinkapambana anzanga ambiri a msinkhu wanga pochita zachiyuda, ndipo ndinali wachangu koposa potsata miyambo ya makolo athu.
15
Koma Mulungu adandipatula ndisanabadwe, ndipo mwa kukoma mtima kwake adandiitana.
16
Tsono pamene adatsimikiza zondiwululira Mwana wake, kuti choncho ndikalalike Uthenga Wabwino wonena za Iye kwa anthu amene sali Ayuda, sindidapite kwa munthu aliyense kuti ndikapemphe nzeru.
17
Sindidapite ngakhalenso ku Yerusalemu kwa anthu amene anali atumwi kale ine ndisanakhale mtumwi. Koma ndidapita ku Arabiya kenaka nkubwereranso ku Damasiko.
18
Pambuyo pake, patapita zaka zitatu, ndidapita ku Yerusalemu kukacheza ndi Petro, ndipo ndidangokhala naye masiku khumi ndi asanu.
19
Sindidaonenso mtumwi wina aliyense kupatula Yakobe yekha, mbale wa Ambuye.
20
Ndikulumbira pamaso pa Mulungu kuti zimene ndikukulemberanizi ndi oona, sindikunama ai.
21
Pambuyo pake ndidakafika ku madera a ku Siriya ndi a ku Silisiya.
22
Koma chonsecho nkuti mipingo yachikhristu ya ku Yudeya isanandiwone ndi kundidziŵa bwino.
23
Inali itangomva mbiri chabe yakuti, “Munthu uja ankatizunza kaleyu, tsopano akulalika chikhulupiriro chimene kale lija ankayesetsa kuchiwononga.”
24
Motero mipingoyi inkalemekeza Mulungu chifukwa cha ine.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6