bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Galatians 4
Galatians 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 5 →
1
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mloŵachuma akali wamng'ono sasiyana ndi kapolo, ngakhale iyeyo ndi mwini chuma chonsecho.
2
Mwanayo ayenera kumvera omulera ndiponso akapitao oyang'anira chuma chake, mpaka nthaŵi imene bambo wake adakhazikitsa.
3
Chimodzimodzinso ifeyo, pamene tinali ana, tinali akapolo a miyambo yapansipano.
4
Koma nthaŵi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose.
5
Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu.
6
Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!”
7
Motero sindiwenso kapolo ai, koma mwana. Ndipo popeza kuti ndiwe mwana wake, Mulungu adakusandutsanso mloŵachuma wake.
8
Kale simunkadziŵa Mulungu, nchifukwa chake munkatumikira zomwe sizili milungu konse.
9
Koma tsopano mukumdziŵa Mulungu, makamaka ndinene kuti Mulungu ndiye akudziŵa inu. Nanga bwanji mukubwereranso ku miyambo yachabe ndi yopanda phindu ija? Bwanji mukufuna kukhalanso akapolo ake?
10
Mumasunga masiku, miyezi, nyengo ndi zaka.
11
Ndikuwopa kuti mwinatu ntchito zanga zonse pakati panu ndidazigwira pachabe.
12
Ndikukupemphani abale, musanduke ngati ine, pakuti inenso ndidasanduka ngati inu nomwe. Simudandilakwire konse.
13
Monga mukudziŵa, pamene ndidayamba kukulalikirani Uthenga Wabwino, ndinkadwala.
14
Ngakhale matendawo anali ngati mayeso kwa inu, komabe simudandinyoze kapena kunyansidwa nane. Kwenikweni mudandilandira ngati mngelo wa Mulungu, kapenanso ngati Khristu Yesu mwini.
15
Nanga chimwemwe chanu chija chili kuti tsopano? Ndikukuchitirani umboni kuti nthaŵi imene ija, kukadatheka, mukadakolowola maso anu nkundipatsa ineyo.
16
Monga ndasanduka mdani wanu popeza kuti ndakuuzani zoona?
17
Anthu amene aja akuchita changu kwambiri pothandiza inu kuti akukopeni, koma changu chaocho sichili chabwino ai. Amangofuna kukupatutsani kuti muzichita changu pakuŵathandiza iwowo.
18
Kwabwino nkumachita changu pa chinthu chabwino masiku onse, osati pokhapokha pamene ndili pamodzi nanu.
19
Inu ana anga, monga mkazi amamva zoŵaŵa pochira, inenso ndikumva zoŵaŵa chifukwa cha inu mpaka moyo wa Khristu ukhazikike mwa inu.
20
Ndikadakonda nditakhala nanu tsopano. Apo kapena ndikadasintha mau anga, chifukwa mwandithetsa nzeru.
21
Inu ofuna kukhala akapolo a Malamulo, tandiwuzani. Kodi simukumvetsa zimene Malamulowo akunena?
22
Paja Malembo akuti, Abrahamu anali ndi ana aamuna aŵiri: wina mai wake anali kapolo, winayo mai wake anali mfulu.
23
Mwana amene mai wake anali kapolo uja, adabadwa monga momwe amabadwira ana onse. Koma mwana wina uja, amene mai wake anali mfulu, adabadwa chifukwa cha lonjezo la Mulungu.
24
Zimenezi zili ngati fanizo. Akazi aŵiri aja akufanizira zipangano ziŵiri. Mmodzi (Hagara uja), ndi wochokera ku phiri la Sinai, ndipo ana ake amakhala akapolo.
25
Hagarayo akufanizira phiri la Sinai la m'dziko la Arabiya, lofanizira Yerusalemu walero, amene ali m'ukapolo pamodzi ndi anthu ake onse.
26
Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mai wathu.
27
Paja Malembo akuti, “Sangalala iwe chumba chosabala ana, imba nthungululu, fuula mokondwera, iwe amene sunamvepo zoŵaŵa za kubala. Ana a mkazi wosiyidwa ndi ochuluka koposa ana a mkazi amene ali naye mwamuna.”
28
Tsono inu abale, ndinu ana a Mulungu chifukwa cha lonjezo lake, monga Isaki.
29
Nthaŵi imeneyo mwana uja amene adaabadwa monga momwe amabadwira ana onseyu, ankasautsa mwana winayo wobadwa mwa mphamvu za Mzimu Woyera, ndipo mpaka tsopano zili chimodzimodzi.
30
Nanga Malembo akuti bwanji? Akuti, “Mpirikitseni kapoloyu pamodzi ndi mwana wake. Mwana wa kapolo asadzakhale konse mloŵachuma pamodzi ndi mwana wa mfulu.”
31
Nchifukwa chake, abale, ife sindife ana a kapolo, ndife ana a mfulu.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6