bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Galatians 5
Galatians 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 6 →
1
Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo.
2
Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai.
3
Ndikufuna kubwerezanso kuuza aliyense woumbalidwa, kuti ayenera kutsata Malamulo onse a Mose.
4
Inu amene mukuyesa kusanduka olungama pakutsata Malamulowo, mudadzipatula nokha kusiya Khristu. Pamenepo mudalekana ndi madalitso aulere a Mulungu.
5
Koma kunena za ife, chifukwa cha kulandira Mzimu Woyera ndiponso pakukhulupirira, tikuyembekeza kuti Mulungu adzatiwona kuti ndife olungama pamaso pake.
6
Pakuti pamene tili mwa Khristu Yesu, kuumbalidwa kapena kusaumbalidwa kulibe kanthu, chachikulu nchakuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi.
7
Munkathamanga bwino lomwe. Tsono adakuletsani ndani kuti musamverenso choona?
8
Kukopeka kwanu kumeneku sikuchokera kwa Mulungu amene amakuitanani.
9
Chofufumitsira chapang'ono chabe chimafufumitsa buledi yense.
10
Ndili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye, kuti simudzakhala ndi maganizo osiyana ndi anga. Koma amene akukusokonezaniyo, ngakhale akhale yani, Mulungu adzamlanga ndithu.
11
Koma kunena za ine, abale, ngati ndikulalikabe kuti anthu aziwumbalidwa, nanga bwanji ndikuzunzidwabe? Ndikadalalikabe kuti anthu aziwumbalidwa, sibwenzi ndikuŵakhumudwitsa pakulalika mtanda wa Khristu.
12
Ndikadakonda kuti amene akukuvutaniwo angodzithena basi.
13
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
14
Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
15
Koma ngati muyamba kulumana ndi kukadzulana, muchenjere kuti mungaonongane kotheratu.
16
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.
17
Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziŵirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita.
18
Koma ngati Mzimu Woyera akutsogolerani, ndiye kuti sindinunso akapolo a Malamulo a Mose.
19
Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,
20
kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,
21
dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.
22
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
23
kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
24
Amene ali ake a Khristu Yesu, adalipachika pa mtanda khalidwe lao lokonda zoipa, pamodzi ndi zokhumba zake ndi zilakolako zake.
25
Ngati Mzimu Woyera adatipatsa moyo, tilolenso kuti Mzimu yemweyo azititsogolera.
26
Tisakhale odzitukumula, oputana, kapena ochitirana dumbo.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6