bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Habakkuk 1
Habakkuk 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
1
Uwu ndi uthenga umene mneneri Habakuku adalandira kwa Mulungu m'masomphenya.
2
Kodi Inu Chauta, ndidzakhala ndikukupemphani chithandizo nthaŵi yaitali bwanji, Inuyo osandiyankha? Kapena kukudandaulirani kuti “Nkhondo kuno,” Inuyo osatipulumutsa?
3
Chifukwa chiyani mukufuna kuti ndiziwona mavuto otereŵa. Chifukwa chiyani mukulekerera zoipa? Ponseponse ndikuwona chiwonongeko ndiponso nkhondo. Pali ndeu ndi kukangana kwambiri.
4
Ndiye kuti malamulo atha mphamvu. Chilungamo sichikugwira ntchito. Anthu oipa akupambana anthu abwino, motero chilungamo chalephereka.
5
Onani mitundu ya anthuyi, muipenyetsetse. Kudzakhala zododometsa ndipo mudzangoti kakasi. Pakuti ndidzachita zinthu zimene simudzakhulupirira mukadzazimva.
6
Ndiye kuti ndidzakweza Ababiloni mtundu woopsa ndi wamphamvu. Iwowo amapita pa dziko lonse lapansi kuti akalande malo a eniake.
7
Kulikonse kumene amapita, amachititsa mantha, amadzipangira okha malamulo, amadzipezera okha ulemu.
8
Akavalo ao ndi aliŵiro kwambiri kupambana akambuku, ndi oopsa kupambana mimbulu yolusa. Okwerapo ao akuthamanga molunjika kuchokera kutali. Akuchita kugudukira ngati chiwombankhanga chofuna kugwira nyama.
9
Gulu lao lankhondo likubwera ndi nkhanza, anthu akuchita mantha iwo asanafike. Amagwira akapolo ochuluka ngati mchenga.
10
Amanyoza mafumu, amanyazitsa atsogoleri. Amapeputsa linga lililonse, poti amangounjika dothi lokwererapo, nalanda mzinda wake.
11
Kenaka amapitirira mofulumira ngati mphepo. Anthuwo amene mphamvu ndiye mulungu wao.
12
Inu Chauta, kodi suja ndinu wachikhalire? Ndinu Mulungu wanga, Woyera wanga uja, wosafa. Inu Chauta, ndinu amene mudaŵasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo pa ife. Inu Thanthwe lathu, mudaŵaika iwowo kuti atilange.
13
Maso anu ndi oyera, safuna kuwona zoipa, simungalekerere anthu ochita uchimo ndi zolakwa. Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu osakhulupirikawo? Bwanji simuchitapo kanthu pamene anthu oipa akuwononga anthu abwino kupambana iwowo?
14
Mumasandutsa anthu kuti azikhala ngati nsomba zam'nyanja, ngati zokwaŵa zimene zilibe wozilamulira?
15
Adani ao amachita ngati kuŵedza anthuwo ndi mbedza, kapena kuŵakola m'kombe. Amaŵakokera m'matchera ao, ndipo amakondwa ndi kusangalala.
16
Tsono amaperekera nsembe makombe ao, ndipo amafukizira lubani matchera ao. Chifukwa zimenezi ndizo zimaŵabweretsera moyo wapamwamba, ndipo amadya bwino.
17
Kodi adzapitirirabe kugwiritsa ntchito makoka ao, ndi kumapha mitundu ya anthu mopanda chifundo mpakampaka?
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3