bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Habakkuk 3
Habakkuk 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
1
Pemphero la mneneri Habakuku potsata maimbidwe a Sigionoti.
2
Inu Chauta, ndamva za mbiri yanu, Inu Chauta, ntchito zanu zandiwopsa. Muzichitenso masiku ano, zikhale zodziŵika makono. Ngakhale muli okwiya, musaiŵale chifundo chanu.
3
Mulungu adabwera kuchokera ku Temani, Woyera uja adabwera kuchokera ku phiri la Parani. Ulemerero wake udaphimba mlengalenga, dziko lonse lapansi linkamutamanda.
4
Adaŵala ngati dzuŵa, kunyezimira kunkatuluka m'manja mwake, m'mene adabisamo mphamvu zake.
5
Kutsogolo kwake kudagwa mliri, kumbuyo kwake kudagwa nthenda yoopsa.
6
Adaimirira ndipo dziko lapansi lidagwedezeka. Adayang'ana ndipo mitundu ya anthu idanjenjemera. Pomwepo mapiri okhazikika adagumuka, ndipo magomo akalekale adatera, njira zake nzachikhalire.
7
Ndidaona anthu a ku Kusani ali pa mavuto, nawonso a ku Midiyani adaagwedezeka.
8
Inu Chauta, kodi mudaakwiyira mitsinje? Kodi mudaakalipira mifuleni? Kodi mudaazazira nyanja? Mutakwera pa akavalo anu mudapambanitsa anthu anu pa nkhondo.
9
Mudasolola uta wanu m'chimake, ndipo mudatulutsa mivi m'phodo lake. Mudang'amba dziko lapansi ndi mitsinje.
10
Mapiri atakuwonani adayamba kugwedezeka. Madzi amphamvu am'mitsinje adasefukira. Nyanja yozama idakokoma, mafunde ake adakwera kwambiri.
11
Dzuŵa ndi mwezi zidangoti jega mu mlengalenga, zitaona kung'anipa kwa mivi yanu, ndi kunyezimira kwa mikondo yanu.
12
Mudayendayenda m'dziko lapansi muli okwiya, mudapondereza anthu a mitundu yonse mwaukali.
13
Mudapita kukapulumutsa anthu anu, mudabwera kudzalanditsa wodzozedwa wanu. Mudakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oipa, mudaonongeratu anthu ake onse.
14
Ndi mivi yanu mudalasa mtsogoleri wa ankhondo ake, amene adaabwera ngati kamvulumvulu kuti atibalalitse. Ankakondwerera ngati kuti akudzaononga osauka mwachinsinsi.
15
Mudapondaponda pa nyanja ndi akavalo anu, ndipo madzi amphamvu adavwanduka.
16
Izi ndazimva, ndipo thupi langa likunjenjemera, m'kamwa fuu chifukwa cha phokosolo. M'mafupa mwazizira, ndipo maondo akuwombana. Ndikudikira tsiku la chilango chimene chidzagwera amene akutithira nkhondo.
17
Ngakhale mikuyu ipande kuchita maluŵa, mipesa ipande kukhala ndi mphesa, mitengo ya olivi ipande kubala zipatso, m'minda musatuluke kanthu, ndipo nkhosa ndi ng'ombe zithe m'khola,
18
komabe kwanga nkukondwerera mwa Chauta, kwanga nkusangalala chifukwa cha Mulungu Mpulumutsi wanga.
19
Ambuye anga, Chauta, ndiwo amandipatsa mphamvu. Amalimbitsa miyendo yanga kuti ikhale ngati ya mbaŵala, kuti ndikafike mpaka pamwamba pa phiri. Kwa Woimbitsa nyimbo. Aimbire zazingwe.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
All chapters:
1
2
3