bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Habakkuk 2
Habakkuk 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
1
Ndidzakhala ngati mlonda, woimirira pa linga. Ndidzaona zimene adzandiwuze, apo ndidzadziŵa zimene adzayankhe za dandaulo langa.
2
Chauta adandiyankha kuti, “Lemba uthengawu, ulembe mooneka bwino pa mapale, kuti woŵerenga aŵerenge mosavuta.
3
Uthengawu ukudikira nthaŵi yake. Nthaŵi yakeyo idzabwera mofulumira, sizidzalephera kuchitika. Ngati ziwoneka kuti zikuchedwa, mudikire. Zidzafika ndithu, si kuchedwa ai.
4
Ochita zoipa adzalephera, koma ochita chifuniro cha Chauta adzakhala ndi moyo chifukwa cha kukhulupirika kwake.
5
Monga munthu wokhuta vinyo ali wosokonezeka, chonchonso munthu wodzitama ndi wosakhazikika. Ndi waumbombo kwambiri ngati manda, ngati imfa amakhala wosakhuta. Amagwira anthu a mitundu yonse, amaŵasonkhanitsa ngati ake.”
6
Koma ogwidwawo adzamnyoza, adzamnyodola ponena kuti, “Tsoka kwa amene amadzikundikira chuma chosakhala chake, amene amalemera ndi ngongole zosalungama. Adzatero mpaka liti?”
7
Angongolewo adzakuukira mwadzidzidzi. Adzakuchititsa mantha ndi kukulanda zako zonse.
8
Chifukwa iweyo udafunkha mitundu yambiri ya anthu, koma otsala adzakufunkha iweyo, chifukwa chokhetsa magazi a anthu ambiri, ndiponso chifukwa choononga mwankhanza mizinda ndi onse okhalamo.
9
Tsoka kwa amene amalemera ndi phindu lobera anzake, kuti akweze malo ake ndi kupewa zovuta.
10
Udafuna kuwononga anthu a mitundu yambiri koma potero wachititsa manyazi banja lako, ndipo wataya moyo wako.
11
Ndi njerwa zomwe za nyumba yako zidzafuula chidzudzulo, ndipo mitanda idzathira mang'ombe ake.
12
Tsoka kwa amene wamanga mzinda pokhetsa magazi, ndipo waukhazikitsa pozunza anthu.
13
Koma Chauta Wamphamvuzonse ndiye watsimikiza kuti zimene anthu amagwirira ntchito zili ngati nkhuni pa moto. Anthu a mitundu yonse amangodzitopetsa popanda phindu.
14
Motero anthu onse adzazindikira ulemerero wa Chauta kuti ndi wodzaza, monga momwe madzi amadzazira nyanja.
15
Tsoka kwa amene amamwetsa anzake zaukali, amene amaŵaledzeretsa kuti aŵachititse manyazi.
16
Koma amene udzachite manyazi ndiwe ndipo onse adzakunyoza kwambiri. Tsopano imwa ndiwe, mpaka kudzandira. Chikho cha chilango cha Chauta chikupeza, ndipo manyazi adzaphimba ulemerero wako.
17
Udzachita mantha chifukwa cha kusakaza nkhalango za ku Lebanoni. Udzaopsedwa chifukwa cha kuwononga nyama zake. Wakhetsa magazi a anthu mwankhanza, waononga mizinda ndi onse okhalamo.
18
Kodi phindu la fano nchiyani? Adalipanga ndi munthu. Ndi chifanizo chabe, ndipo nchinthu chonyenga. Munthu wopangayo amakhulupirira zimene wachita, koma mafano akewo satha nkulankhula komwe.
19
Tsoka kwa amene amauza mtengo kuti, “Nyamuka!” Amene amauza mwala waduu kuti, “Dzuka!” Kodi zimenezi zingathe kulangiza? Nzopangidwa ndi golide ndi siliva, ndipo sizitha konse kupuma.
20
Koma Chauta ali m'Nyumba yake yoyera. Dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3