bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joel 1
Joel 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
1
Nawu uthenga umene Chauta adapatsa Yowele, mwana wa Petuwele:
2
Inu akuluakulu, mverani. Tcherani khutu, inu nonse okhala m'dziko. Kodi zoterezi zidaonekapo nthaŵi yanu kapena nthaŵi ya makolo anu?
3
Muŵauze ana anu, iwowo auze ana ao, ndipo anawo aziwuzanso ana ao.
4
Chimene chiwala chidasiya, dzombe lidadya. Chimene dzombe lidasiya, mandowa adadya, chimene mandowa adasiya, chilimamine adadya.
5
Dzukani inu zidakwa, ndipo mulire. Mulire modandaula inu nonse okonda vinyo: mphesa zotchezera vinyo watsopano zaonongedwa,
6
Chikhamu cha dzombe chagwa m'dziko lathu nchamphamvu ndiponso chosaŵerengeka. Mano ake ali ngati a mkango wamphongo, zibwano zake ngati za mkango waukazi.
7
Aononga mpesa wanga, athyolathyola mitengo yanga ya mikuyu. Aisadza, aikungunula makungwa, naŵataya, nthambi zake nkumazisiya zili mbee.
8
Inu anthu, lirani kwambiri ngati namwali wovala chiguduli. Wolira chifukwa cha imfa ya mnyamata wofuna kumkwatira.
9
Chopereka cha chakumwa ndi cha chakudya siziperekedwanso ku Nyumba ya Chauta. Ansembe akulira, atumiki a Chauta aja.
10
Minda yaguga, nthaka ikulira poti tirigu waonongeka, mphesa zaumiratu, mitengo ya mafuta yauma.
11
Tayani mtima, inu alimi, lirani, inu olima mphesa, chifukwa tirigu ndi barele, ndi zonse zam'minda zalephera.
12
Mpesa wauma, mkuyu wafota. Mkangaza, kanjedza, mitengo ya apulosi ndi mitengo yonse ya m'dziko yaumiratu. Choncho chikondwerero cha anthu chatheratu.
13
Inu ansembe, valani ziguduli mudzigunde pa chifuwa chifukwa cha chisoni. Lirani, inu otumikira ku guwa. Tiyeni, mufunde ziguduli usiku wonse, inu atumiki a Mulungu wanga. Pakuti chopereka cha chakudya ndi chakumwa sizidzaonekanso ku Nyumba ya Mulungu wanu.
14
Lamulani kuti anthu asale zakudya. Itanitsani msonkhano waulemu. Akulu ndi onse okhala m'dziko asonkhane ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, ndipo iwowo alire kwa Iye.
15
Kalanga ine! Tsiku loopsa layandikira, tsiku la Chauta, likubwera ndi chiwonongeko chochokera kwa Mphambe.
16
Chakudya chathu chikutha ife tikuwona. Mulibenso chimwemwe ndi chisangalalo m'Nyumba ya Mulungu wathu.
17
Mbeu zakongonyala, poti pansi mpouma. Nyumba zosungiramo dzinthu zaonongeka, nkhokwe zapasuka, popeza kuti zokolola palibe.
18
Zoŵeta zikulira ndi njala. Ng'ombe zikungoyenda uku ndi uku chifukwa choti zilibe busa. Nazonso nkhosa zikusauka.
19
Ndikulira kwa Inu Chauta, pakuti moto wapsereza mabusa akuthengo, ndipo malaŵi a moto apsereza mitengo yonse yam'tchire.
20
Nazonso nyama zakuthengo zikulira kwa Inu, chifukwa timitsinje tonse taphwa, ndipo moto wapsereza mabusa akuthengo.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
Recommended Reading
Commentary
Joel Commentaries
→
Devotional
Joel Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→