bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joel 3
Joel 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
1
“Nthaŵi imeneyo itafika, masiku amene ndidzakwezanso anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu,
2
ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu a mitundu yonse, ndipo ndidzaŵatengera ku chigwa cha Yehosafati. Kumeneko ndidzaŵaweruza chifukwa cha zimene adachitira Aisraele, osankhidwa anga, pakuti adaŵamwaza m'maiko ao onse, nagaŵana dziko langa.
3
Adagaŵana anthu anga pochita maere, mnyamata adamsinthitsa ndi mkazi wadama, mtsikana nkumsinthitsa ndi vinyo, kenaka adamumwa vinyoyo.
4
“Kodi inu a ku Tiro, a ku Sidoni ndi a ku madera a Filistiya, mukuti mundichite chiyani? Kodi mumati mundilipsirire chifukwa cha zina zimene ine ndakuchitani? Ngati pali kanthu koti mundilipsirire, ndidzabwezera zochita zanu zonse pamutu panu mofulumira.
5
Inu mudatenga siliva ndi golide wanga ndi zinthu zanga zina zamtengowapatali, kupita nazo ku nyumba za milungu yanu.
6
Mudakagulitsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kwa Agriki, kuti mupite nawo kutali ndi malire a dziko lao.
7
Koma ndidzaŵadzutsa kuti achoke kumalo kumene mudaŵagulitsa. Kenaka ndidzabwezera zochita zanu zonse pamutu panu.
8
Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a ku Yuda, ndipo iwo adzaŵagulitsa kwa Aseba, mtundu wa anthu okhala kutali aja. Ndatero Ine Chauta.
9
“Mulengeze pakati pa anthu a mitundu ina kuti, ‘Konzekerani nkhondo, itanani ankhondo amphamvu. Asilikali onse afike pafupi, ayambe nkhondo.
10
Sulani makasu anu kuti akhale malupanga. Sulani migwandali yanu kuti ikhale mikondo. Ngakhale wofooka anene kuti, Ndalimba mtima.
11
“ ‘Fulumirani, bwerani, inu anthu a mitundu yonse yozungulira, ndipo musonkhane kumeneko.’ ” Inu Chauta, tumizani ankhondo anu.
12
“Anthu a mitundu yonse akonzeke ndipo abwere ku chigwa cha Yehosafati. Pakuti kumeneko ndidzaweruza anthu a mitundu yonse, ochokera ku mbali zonse.
13
“Samulani zenga wodulira tirigu, pakuti mbeu zacha kale kudikira kholola. Bwerani, dzapondeni mphesa, poti mopondera mphesa mwadzaza, ndipo mbiya zikusefukira. Chonchonso zolakwa za mitundu ina ya anthu zachuluka zedi.”
14
Makamu ndi makamu a anthu ali m'Chigwa cha Chiweruzo. Ndithu tsiku la Chauta layandikira m'Chigwa cha Chiweruzo.
15
Dzuŵa ndi mwezi zada, ndipo nyenyezi zaleka kuŵala.
16
Chauta akukhuluma ku Ziyoni, mau ake amveka ngati bingu kuchokera ku Yerusalemu. Ndipo thambo ndi dziko lapansi zikugwedezeka. Koma Chauta ndiye pothaŵirapo anthu ake, ndiye linga lotetezera a ku Israele.
17
“Motero mudzadziŵa kuti ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndimakhala ku Ziyoni, ku phiri langa loyera. Yerusalemu adzakhala woyera ndipo alendo sadzamthiranso nkhondo.
18
“Nthaŵi imeneyo ikadzafika, mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndipo kuzitunda kudzayenderera mkaka. Mitsinje yonse ya ku Yuda idzadzaza ndi madzi. Kasupe adzatumphuka ku Nyumba ya Chauta ndi kuthirira chigwa cha Sitimu.
19
“Koma Ejipito adzasanduka chipululu, ndipo Edomu adzakhala bwinja lopanda anthu, chifukwa cha nkhondo imene adathira pa anthu a ku Yuda ndiponso chifukwa cha kukhetsa magazi a anthu osalakwa ku dziko lao.
20
Koma ku Yudako kudzakhala anthu mpaka muyaya, ndipo ku Yerusalemu sikudzatha anthu pa mibadwo yonse.
21
Ndidzalipsira magazi a ophedwawo, sindidzalekerera tchimo la olakwawo. Ine Chauta ndimakhala ku Ziyoni.”
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
All chapters:
1
2
3