bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Joel 2
Joel 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
1
Lizani lipenga ku Ziyoni. Fuulani mochenjeza pa phiri langa loyera. Onse okhala m'dziko anjenjemere, pakuti tsiku la Chauta likufika, layandikira.
2
Ndi tsiku lamdima ndi lachisoni, tsiku lamitambo ndi la mdima wandiweyani. Gulu la ankhondo amphamvu ochuluka langoti bii ngati mdima wokuta mapiri. Gulu lotere silinaonekepo nkale lonse, ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso.
3
Kutsogolo kwake moto ukupsereza, kumbuyo kwake malaŵi a moto akutentha zinthu. Iwo asanafike, dziko linali ngati munda wa Edeni, koma atachoka, lidasanduka chipululu! Palibe kanthu kotsalapo.
4
Maonekedwe ake ali ngati a akavalo, liŵiro lake ngati la akavalo ankhondo.
5
Akulumpha pamwamba pa mapiri ndi phokoso longa la magaleta. Akumveka ngati malaŵi a moto otentha ziputu, ngati gulu lamphamvu lankhondo litakonzekera kumenya nkhondo.
6
Anthu a mitundu ina amachita mantha akaŵaona, nkhope zonse zimatumbuluka.
7
Akududuka ngati ankhondo. Akukwera malinga ngati asilikali. Aliyense akuyenda pa mzere, osasempha njira yake.
8
Sakukankhanakankhana, aliyense akuyenda molunjika. Akupyola pakati pa zida zankhondo, osaŵaimitsa.
9
Akuulumphira mzindawo, akukwera pamwamba pa malinga. Akuloŵa m'nyumba, akuloŵera pa windo ngati mbala.
10
Dziko lapansi likugwedezeka pamene iwo akuyandikira. Mlengalenga ukunjenjemera. Dzuŵa ndi mwezi zikuchita mdima, ndipo nyenyezi zikuleka kuŵala.
11
Chauta akumveketsa liwu lake kutsogolo kwa gulu lake lankhondo. Gulu lake lankhondolo ndi lalikulu kwambiri. Wochitadi zimene Chauta akulamula, ngwamphamvu. Tsiku la Chauta ndi lalikulu ndi loopsa. Ndani angathe kupirira tsikulo?
12
Koma Chauta akunena kuti, “Ngakhale tsopano bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse, mukusala zakudya, mukukhetsa misozi ndi kulira mwachisoni.
13
Ng'ambani mitima yanu, osati zovala zanu chabe.” Bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika. Nthaŵi zonse ndi wokonzeka kukhululuka.
14
Mwina mwake adzasintha mtima ndi kuleka, ndipo adzatisiyira madalitso. Madalitsowo adzakhala a chopereka cha chakudya ndi chakumwa zopereka kwa Chauta, Mulungu wanu.
15
Lizani lipenga ku Ziyoni. Lengezani mwambo wa kusala zakudya. Muitanitse msonkhano waukulu.
16
Sonkhanitsani anthu pamodzi, muŵauze kuti adziyeretse. Sonkhanitsani akuluakulu, sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Lamulani kuti nawonso akwati achoke m'chipinda mwao, abwere.
17
Ansembe, amene ali atumiki a Chauta, azilira pakati pa guwa lansembe ndi khonde. Azinena kuti, “Inu Chauta, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti ena aŵanyoze anthu anu osankhidwa. Anthu achikunja asaŵaseke pomafunsana kuti, ‘Ha, ali kuti Mulungu waoyo?’ ”
18
Apo chikondi cha Chauta chidayaka ngati moto chifukwa cha dziko lake, ndipo adaŵachitira chifundo anthu ake.
19
Chauta adaŵayankha anthu ake kuti, “Ndikutumizirani tirigu, vinyo ndi mafuta, ndipo mudzakhuta ndithu. Sindidzalolanso kuti akunja akunyozeni.
20
Ndidzachotsa adani akumpoto kuti akhale kutali ndi inu, ndipo ndidzaŵapirikitsira ku dziko louma ndi lachipululu. Akutsogolo ndidzaŵathamangitsira ku nyanja yakuvuma, akumbuyo ndidzaŵathamangitsira ku nyanja yakuzambwe. Tsono mitembo yao idzatulutsa chivundi ndi fungo lonunkha. Zoonadi Chauta adachita zazikulu.
21
“Iwe dziko, usachite mantha. Kondwa ndipo usangalale, pakuti Chauta mwini wake adachita zazikulu.
22
Inu nyama zakuthengo, musaope, pakuti msipu wakuchipululu akuphukira. Mitengo ikubala zipatso. Mkuyu ndi mpesa zikubereka kwamphamvu.
23
“Inu anthu a ku Ziyoni, kondwani ndi kusangalala chifukwa cha zimene Chauta, Mulungu wanu, wakuchitirani. Wakukomerani mtima pokupatsani mvula mofulumira. Wakupatsani mvula yochuluka, kumayambiriro ndi kumathero, monga pa masiku amekedzana.
24
“Pa malo opunthira padzadzaza tirigu. Mopondera mphesa mudzasefukira vinyo watsopano, mafutanso adzachuluka.
25
Motero ndidzakubwezerani zonse zimene zidaonongedwa ndi dzombe, mandowa, mphutsi ndi ziwala. Limenelitu ndiye gulu lankhondo lija limene ndidatuma kudzakukanthani.
26
“Mudzadya zambiri ndi kukhuta, ndipo mudzatamanda dzina la Chauta, Mulungu wanu, amene wakuchitirani zodabwitsa. Choncho anthu anga sadzaŵanyozanso ai.
27
Mudzadziŵa kuti Ine ndili naye Israele, ndipo kuti Ine ndekha, osati wina, ndine Chauta, Mulungu wanu. Anthu anga sadzaŵanyozanso ai.
28
“Patapita nthaŵi, tsiku lidzafika pamene ndidzatsitsa mzimu wanga pa mtundu uliwonse wa anthu. Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzalosa. Nkhalamba zanu zidzalota maloto, ndipo achinyamata anu adzaona zinthu m'masomphenya.
29
Masiku amenewo, ndidzatsitsa mzimu wanga ngakhale pa akapolo ndi pa adzakazi omwe.
30
“Mu mlengalenga ndi pa dziko lapansi ndidzaonetsa zodabwitsa izi: magazi, moto ndi utsi watoloo.
31
Dzuŵa lidzasanduka mdima, ndipo mwezi udzasanduka magazi, tsiku lalikulu ndi loopsa la Chauta lisanafike.
32
Ndipo aliyense amene adzatama dzina la Chauta mopemba, adzapulumuka. Monga Iye adanenera, kudzakhala ena opulumuka ku phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo mwa otsalawo padzapezeka ena amene Chauta adzaŵaitana.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3