bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jonah 2
Jonah 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 3 →
1
Tsono Yona ali m'mimba mwa chinsomba chija, adayamba kutama Chauta mopemba.
2
Adati, “Inu Chauta, pamene ndinali m'mavuto ndidakuitanani, ndipo mudandiyankha. Pamene ndinali m'dziko la akufa ndidalira kwa Inu kuti mundithandize, ndipo mudamva pempho langa.
3
Mudandiponya m'nyanja yozama, m'kati mwenimweni mwa njanja, ndipo mweza wam'nyanjamo udandizungulira.
4
Pamene ndidati, ‘Mwanditaya kutali ndi Inu. Kodi ndidzaiyang'ananso bwanji Nyumba yanu yoyera?’
5
Madzi adandiyesa m'khosi, nyanja yozama idandizungulira. Udzu wakayandeyande udandikwidzinga m'mutu.
6
Ndidatsikira kunsi ndithu, m'tsinde mwa mapiri, kudziko kumene mipiringidzo idanditsekera mpaka muyaya. Koma Inu Chauta, Mulungu wanga, mudanditulutsa kumandako ndili moyo.
7
Poona kuti ine nkufatu kuno, ndidakumbukira Inu Chauta, pemphero langa lidakufikani m'Nyumba yanu yoyera.
8
Anthu opembedza milungu yachabe amataya kukhulupirika kwao.
9
Koma ine ndidzapereka nsembe kwa Inu ndi mau okuthokozani. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita ndithu. Chipulumutso nchochokera kwa Inu Chauta.”
10
Apo Chauta adalamula chinsomba chija kuti chisanzire Yona ku mtunda.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4