bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jonah 3
Jonah 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
1
Chauta adalankhula ndi Yona kachiŵiri, namuuza kuti,
2
“Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukulu uja, ukaulalikire uthenga umene ndikukuuza.”
3
Yona adanyamuka, napita ku Niniveko, potsata mau a Chauta. Mzindawo unali waukulu kwambiri, wofunika masiku atatu kuudutsa.
4
Yona adaloŵa mumzindamo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Adayamba kulalika kuti, “Pakapita masiku makumi anai, Ninive aonongeka!”
5
Anthu a ku Ninive adakhulupirira Mulungu. Adalengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamng'ono yemwe, asale zakudya, ndipo avale chiguduli.
6
Mfumu ya ku Ninive itamva zimenezo, idatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake. Idavala chiguduli, nikakhala nao pa dzala.
7
Tsono mfumuyo idalengeza ku Ninive, kuti, “Nali lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: ‘Munthu aliyense asadye kanthu, ndiponso ziŵeto zonse zikuluzikulu ndi zing'onozing'ono zomwe zisadye kanthu. Zisadyetu kanthu, nkumwa madzi komwe zisamwe.
8
Anthu avale ziguduli, nyamanso aziveke ziguduli. Anthuwo azifuula kwa Mulungu ndi mphamvu zao zonse. Ndithu aliyense asiye makhalidwe ake oipa ndi ntchito zake zankhanza.
9
Nkudziŵanji, mwina Mulungu nkutikhululukira, naleka kutikwiyira, ifeyo osaonongeka.’ ”
10
Mulungu adaona zimene anthuwo adachita, ndi m'mene adasiyira makhalidwe ao oipa. Choncho adakhululuka, osaŵapatsa chilango chimene adaati adzaŵapatsa.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4